Bambo ali mchitokosi pa mulandu ogwirilira mwana wa zaka 8

Advertisement

Apolisi m’boma la Balaka amanga bambo wina, a Goodson Ali, a zaka 18 powaganizira kuti adagwirilira mwana wa zaka zisanu ndi zitatu (8).

Malingana ndi wachiwiri kwa mneneri wa polisi ya Balaka, Mphatso Munthali, bamboyu adachita izi pa 2 September, 2023 m’mudzi mwa Kambadi m’boma lomweli la Balaka.

A Munthali adati bambo oganizilidwayu akuti adapempha mwanayu kuti awapelekeze kumunda wawo wa mtedza komwe akuti adachita zamalodzazi.

A Munthali adawonjezera kuti bamboyu adapeleka ndalama yokwana K50 kwa mwanayu ngati chitsekapakamwa.

Komabe, mwanayu atafika kunyumba adawulura za malozadzi kwa mai ake.

Ndipo zotsatira za chipatala zomwe adachita madotolo a pachipatala chachikulu cha Balaka zidatsimikiza kuti mwanayu adagonedwadi.

Bambo oganizilidwayu yemwe amachokera m’mudzi mwa Kambadi, mfumu yaikulu Nsamala m’boma la Balaka akawonekera ku bwalo la milandu posachedwapa kukayankha mlandu ogwirilira mwana zomwe ndi zosemphana ndi gawo 138 la mmalamulo oyendetsera dziko lino.

Advertisement