Bambo wa zaka 27 amumanga chifukwa chogwirilira mnyamata

Advertisement
Rape suspect Chimkute arrested by Malawi Poloce

Bambo wa zaka 27 yemwe dzina lake ndi Makaiko Moyo Chimkute amumanga ku Mchinji chifukwa chogwirilira mwana wa zaka 14.

Malingana ndi wofalitsa nkhani za apolisi ku Mchinji a Limbani Mpinganjira, anthu awiri-wa anayamba kucheza pa tsamba la facebook ndipo dzulo bamboyo anayitana mnyamatayo kunyumba kwake pomulonjeza kuti amugulira zakumwa zoziziritsa ku khosi.

Pa 5 September, mwanayo anapita kunyumba ya Chimkute komwe oganizilidwayo adamunyengerera mwanayo ndi bisiketi wa vanilla koman chakumwa cha Yes.

Ali komweko, Chimkute anayamba kumupsopsona mwanayo uku akumugwira kumalo obisika.

Chimkute anamugwirilira mwanayo kudzera malo ochitira chimbudzi.

Atachoka kwa a Chimkute mwanayo anakanena kwa makolo ake omwe adakatula nkhaniyi ku polisi.

Apolisi adagwira woganiziridwayu amene akuyembekezera kukaonekera kubwalo la la milandu.

Chimkute amachokera m’mudzi wa Simphasi mdera la mfumu yayikulu Chaima m’boma la Kasungu.

Kugonana ndi mwana aliyense wa zaka zosafika 18 ndikugwirilira ngakhale mwanayo atavomera chifukwa mwana sangakwanitse kupanga chiganizo choyenera chokhudza zogonana. Munthu wamkulu opezeka akugonana ndi mwana amakhala walakwira malamulo ndipo atha kumugamula kukakhala ku ndende moyo wake onse.

Advertisement