Kodi munthu nkukhala yekha? Driemo wazula wake pa Zambia

Advertisement
Chichi Dasiy Driemo Malawi

Ba neba kumatipatsa ulemu ndife amuna anu: Oyimba yemwe watekesa pa Malawi Driemo, watutumutsa gulu pomwe zikumveka kuti wazula wake pa Zambia.

Nkhaniyi yadziwika lachinayi pa 24 August pomwe oyimbayu yemwe watenga chikoka cha anthu ochuluka m’dziko muno komaso mayiko ozungulira makamaka azimai, anaika zithuzi za mkazi oganizilidwayu pa tsamba la nchezo.

Driemo anaika zithuzi za nyenyeziyi pa tsamba lake la tiktok koma sanalembe kalikose kupatula dzina la mkaziyu yemwe akudziwika kuti Chichi Daisy Lupsy, yemwe amakhalapo m’dzikola Zambia.

Zithunzi zomwe anaika oyimbayu zabweretsa manong’onong’o m’masamba a nchezo ndipo anthu akuyankhula zosiyanasiyana; ena kuyamikira kuti oyimba wathuyu watichotsa manyazi pamene ena akunyoza nthiti ya katswiri wathuyu.

Anthu ena akudandaula kuti nchifukwa chiyani oyimbayu wapita mpaka m’dziko la Zambia kukasaka mlamwathuyo chosecho m’dziko muno maluwa owoneka bwino, osafota alipo ochuluka zedi.

“ETI akazi onsewa ali mmalawi munowa, ENA akuchita kukwera mapiri maondo kusupuka kupempha mwamuna wa banja,basitu chipongwe chake Driemo kukapeza mkazi wa ku Zambia yemwe akumutcha Chichi Daisy,” latelo tsamba lina pa fesibuku.

Enaso zoti chikondi ndi m’maso ndipo ayamba kudzudzula oyimba Driemo kaamba kofusira nkazi yemwe a kuti akuoneka wamkulu kuyelekeza ndi sayizi ya oyimba wathuyu.

“Nayeso kusaona size ngati amuna aku joni bwanji..? Koma naye nde wazitengera chi mama,” atelo anthu awiri poyikira ndemanga pa tsamba lina pa fesibuku.

Mbali inayi ena akuyamikira kuti Driemo wapeza nkazi owala ndipo amulangiza kuti asamutaye ponena kuti awiriwa akukhalana ndipo angapange banja labwino.

“Mwanayu watchukitsitsa ndipo amangoyenera kupeza mkazi okongola chonchi, congratulations oyimba wathu, uku nde kubwera, musamvere za enawa maso chitsogolo basi, tidumphe masipika ife,” watelo munthu wina.

Ena ati nzosadabwitsa kuti oyimba Driemo wapeza nthiti yake m’dziko la Zambia kaamba koti oyimbayu anaonetsa kale kuti ali paubale wabwino ndi anthu a m’dzikoli pomwe chimbale chaka cha Mzaliwa, Driemo waimba ndi oyimba ambiri a m’dzikolo.

Koma ngakhale zosezi zili choncho, nzosatsimukizika ngati awiriwa alidi m’chikondi.

Advertisement