Zina ukamva: Bambo adula mutu wa nkazi ndi mwana kenaka nkudzikhweza

Advertisement

Bambo wa zaka 27 m’boma la Karonga wadabwitsa anthu pomwe wadula mutu wa nkazi komaso mwana wake kenakaso naye nkudzimangilira.

Izi ndi malingana ofalitsa nkhani pa polisi ya Karonga a George Mulewa omwe azindikira bamboyu ngati Jonathan Mzumara omwe apha nkazi wawo Mervis Kumwenda komaso mwana wawo Ian Mzumara.

A Mulewa ati nkhaniyi yachitika kumayambiliro kwa sabata ino m’dera lotchedwa Kambwe m’boma lomwelo la Karonga.

A polisi ati anthu omwe amadutsa pa nyumba ya Mzumara, anadabwitsika ndifungo komaso ntchentche zomwe zimaulukauluka pa nyumbayi.

Izi zinachititsa kuti anthu ayitanizane ndipo gulu la anthu lomwe linakhamukira pa malowa linangoti kukamwa yasa litapeza kuti eni ake anyumbayi onse anali mitembo.

Apolisi ati matupi a nkazi komaso mwana wa m’banjali anapezeka pa balanda ali magazi okhaokha komaso mitu yawo itadulidwa pamene thupi la bambo Mzumara linapezeka litamangililidwa kudenga kwa nyumbayo.

A Mulewa atiso zotsatira za chipatala omwe anayeza matupiwa zaonetsa kuti mkazi ndi mwana wa Mzumara amwalira kamba kotaya magazi ochuluka kamba kodulidwa mitu, ndipo Mzumara wafa kamba kobanika.

Malipoti osatsimikizika akuonetsa kuti mu banjamu mwakhala muli kusamvana ndipo awiriwa akhala akukangana kuchokera mchaka cha 2019.

Mervis Kumwenda mkazi wa Jonathan anali ndi zaka 21 pamene mwana wawo, Ian Mzumara anali ndi zaka ziwiri zakubadwa.

Advertisement