Bambo wafa mgodi wa golide utadilizika ku Kasungu

Advertisement

Bambo wa zaka 45 wafa m’mudzi wa Maluzi ku Kasungu atakwililika mu mgodi omwe amakumbamo golide.

Bamboyu dzina lake ndi Godfrey Chirombo.

Malingana ndineneri wa polisi ya Kasungu, Sub-Inspector Jospeh Kachikho, a Chirombo pamodzi ndi mwana wawo analowera ku mtsinje wa Chithimbiri womwe uli m’deralo kuti akafukule mwala golide

Mwana wawoyo anawasiya kaye a Chirombo komweko iye ndikulowera ku nyumba kwawo kuti akapange kaye zina ndipo akuyendera chapatali anaona kuti dzenje lomwe bambo akewo analowa lagumukira mkati.

Ataona izi, anayitaniza anthu omwe anali pafupi kuti afukule thupi la bambo akewo koma mwatsoka anapezeka atamwalira kale.

Zotsatira za chipatala zasonyeza kuti a Chirombo anamwalira kamba kosowa mpweya.

Advertisement