Ace Jizzy, Bee Jay akana K12m kuti ayambe kuyiba nyimbo zauzimu

Advertisement

Oyimba nyimbo za hipapu Ace Jizzy komaso Bee Jay, akana K12 miliyoni yomwe malume awo anati awapatsa ngati awiriwa angavomere kusiya kuyimba nyimbo za chikunja ndikuyamba kuyimba nyimbo zauzimu.

Malume a anyamatawa a Israel Ndelezina omwe ndi mtumiki wa Mulungu, analemba patsamba lawo la nchezo la fesibuku kufotokoza za khumbo lawo loti Ace Jizzy komaso Bee Jay asiye kuyimba nyimbo za chikunja ndipo ayambe kutumikira Mulungu mmaitanidwe.

Ndelezina anapitilira ndi kufotokoza kuti zimawakhudza kuti pamene iwo amakhala akukangalika kufalitsa uthenga wabwino kwa anthu ena, azibale awo amakhala akuchita kusaweluzika zomwe anati akufuna zithe.

Mkuluyu anapeleka sabata imodzi kwa oyimbawa kuti akhale atapanga chiganizo pa nkhaniyi ndipo analonjeza kuti ngati oyimbawa angalore, adzawathandiza powapatsa ndalama yokwana K12 miliyoni.

“Ndine wokonzeka kuwapatsa ndalama zochulukirapo kuti akajambule nyimbo ngati ali okonzeka kuyamba kuyimba nyimbo za uthenga wabwino kuti afotokoze kuchuluka kwa nkhawa zanga komanso chikhulupiliro changa chonse pakutha kwawo kukhala ndi zotsatira zabwino.

“Ndikuwapatsa sabata imodzi kuti aganize bwino ndipo ndikuyembekeza kuti mutenga nthawi kuti muganizire za chikoka ndi mphamvu zomwe muli nazo ngati oyimba,” anatelo Ndelezina muuthenga wake kwa Ace Jizzy ndi Bee Jay.

Koma poyankha kwawo kudzera pa tsamba lawo la fesibuku, oyimbawa ati sali okozeka kusiya kuyimba nyimbo za chikunja ndikuyamba kuyimba nyimbo za uzimu monga mwa kupempha kwa malume awo a Ndelezina.

Awiriwa ati apanga chiganizochi polingalira komwe achokera pankhani ya mayimbidwe koma atsindika kuti chiganizo chawo sichikutanthauza kuti samakhulupilira Mulungu ponena kuti chikhulupiliro chawo anayika mwa Mulungu kalekale chifukwa anakulira m’mabanja la chikhristu.

“Titalingalira bwino za nkhaniyi komaso kufusa maganizo kwa anthu ena omwe amazitsata za mayimbidwe, tapanga chisankho chogwirizana ndi zimene timakhulupirira kwambiri. Ndi ulemu waukulu ndi chiyamiko, tasankha kukana zoperekedwa ndi a malume athu a Israel kuti tiyambe kuyimba nyimbo za uzimu.

“M’malo mwake, tasankha kukhala owona ku njira yanyimbo yomwe takhala tikudzipangira mwakhama. Tikufuna kutsindika kuti chisankho chimenechi si chisonyezero cha kukayikira kulikonse m’chikhulupiriro chathu kapena kusakhulupirira Mulungu. Zosiyana kwambiri. Chikhulupiriro chathu chimakhalabe chokhazikika,” atelo oyimba awiri wa.

Ace Jizzy komaso Bee Jay, ati akuona kuti n’kofunika kwambiri kuti mfundo zimene akuliramo zizionekera m’nyimbo zawo zomwe amayimba pano zomwe akuti zakhala zikupeleka kale uthenga wa bwino kwa anthu ochuluka.

“Talemba nyimbo zamitundu yosiyanasiyana, kuyambira zolimbikitsa ena kuti apambane, zokondwerera moyo mpaka kuphunzitsa. Tikufuna kuwalimbikitsa, kuwapatsa chiyembekezo, kuwasangalatsa, ndi kuwaphunzitsa anthu mfundo zofunika za choonadi kudzera m’nyimbo zathu,” anaonjezera choncho oyimbawa.

Awiriwa anamaliza ndi kuthokoza anthu onse powagwira dzinja nthawi zonse kuti afike pomwe ali pano ndipo alonjeza kupitilira kuyimba nyimbo zabwino za chikunja.

Advertisement