Boma alipempha kuti likonze msewu ndi mlatho wa Chapananga

Advertisement

Phungu wamdera la Chikwawa West Susan Dossi wati kuwonongeka kwa msewu ndi mlatho wa Chapananga kwapangitsa kuti anthu amdera lake adzivutika kwambiri pamoyo wawo wa tsiku ndi tsiku.

Dossi wauza Malawi24 kuti anthu amdera lake akuvutika kupeza thandizo la za umoyo, alimi akuvutika kukagulitsa zokolola zawo komanso kugula feteleza chifukwa chakuwonongeka kwa msewu ndi mlatho.

Iye wati mlatho wa Chapananga udakokoloka ndi madzi chaka cha 2021 ndipo Boma lidalonjeza kuti msewu ayamba kuwukonza mwezi uno wa June koma mpaka pano palibe chomwe chikuchitika chosonyeza kuti msewu ayamba kuwokodza posachedwa.

Pamenepa Phunguyu wati alindi nkhawa kuti alimi avutikanso kugula fetereza chaka chino chifukwa chavuto la mlatho komanso ana a sukulu adzizavutika nyengo ya mvula ikafika.

“Ndipemphe Bungwe la National Roads Authority (NRA) kudzera ku Unduna wa zamtengatenga ndi zomanga manga (Ministry of Transport and Bublic Infrastructure) kuti atikonzere nseu komanso mlatho wa Chapananga chifukwa anthu akuzunzika,” anatero Susan Dossi.

Boma la Chikwawa ndi limodzi mwama boma omwe Namondwe wa Freddy adaononga  kwambiri chaka chino komanso chaka chilichonse limakhudzidwa ndikusefukira kwa madzi.

Follow us on Twitter:

Advertisement