Samalani mbatatayo ndi dilu – watelo katswiri wa zaulimi

Advertisement

Pamene anthu m’dziko muno akuchita nthabwala ndi kuchuluka kwa mbatata ya kholowa yomwe siyinasiye malo, katswiri wina wa zaulimi walangiza anthu komaso alimi kuti asamale kwambiri chakudyachi.

Kwa ka nthawi tsopano, anthu ochuluka m’dziko muno makamaka m’masamba a nchezo, akukambilana za mpweche wa mbatata omwe dziko la Malawi ladalitsika nawo.

Ena akunyogodola kuchuluka kwa mbatatazi m’dziko muno pomanena kuti kudya katatu komwe atsogoleri a mgwirizano wa Tonse analonjeza nthawi yokopa anthu, kwayamba kutheka chifukwa chakupezeka kwa mbatatazi.

Mbali inayi, zithunzi za chakudyachi sizinasiye malo m’masamba a nchezo ochuluka, kwinaku tinkhani toseketsa tokhudza chakudyachi tikumakhala tikuyenda m’magulupu ambiri.

“Munthu kudwala kukayezetsa kukupeza ndi nthenda ya mbatata yambiri mthupi,” anatelo mlakatuli Robert Chiwamba pa tsamba lake la fesibuku.

Komatu nthabwala komaso mnyozo omwe mbatatazi zikulandira zili apo, katswiri pa nkhani za ulimi a Ronald Chilumpha walangiza anthu m’dziko muno makamaka alimi kuti asamale bwino chakudyachi.

A Chilumpha anauza imodzi mwa nyumba zofalitsira mawu m’dziko muno kuti pomwe pali chiopsezo choti m’dziko muno mukhala njala yadzaoneni, nkofunika kwambiri kusamalira kwambiri mbatata yomwe ikuoneka kuti siyinasiye malo.

Iwo ati anthu akuyenera kugwiritsa ntchito njira zomwe zingapangitse kuti mbatatazi zisungidwe kwa nthawi yaitali ndi cholinga choti njala ikadzayamba, mbatatazo zidzalowe mmalo mwa chimanga chomwe sichinachite bwino m’madera ochuluka.

A Chilumpha anapitiliza ndikulangiza adindo m’dziko muno kuti ayambe kulingalira njira zamakono zomwe zingapititse patsogolo ulimi wa mbewuyi ponena kuti uwu ndi ulimi omwe utha kupindulira dziko lino.

Iwo anapeleka chitsanzo kuti patakhala njira zabwino, m’dziko muno mutha kuyamba kupangidwa ufa ochokera ku mbatata omwe ati utha kumagwiritsidwa ntchito m’dziko muno komaso wina kumatumiza mayiko akunja zomwe ati zitha kukwezaso chuma cha dziko lino.

Izi zikubwera kaamba koti mmadera ambiri mdziko muno mvula yasiya kubwera mochedwelako zomwe zapangitsa kuti mbatata ichite bwino kuposa mbewu zina monga chimanga.

Njira zina zosungira mbatata kuti idzadyedwe mtsogolo, ndi monga kuyikwilira m’dzenje lomwe limatchedwa nkhuti, komaso madera ena amayisenda ndikuyiyanika kuti iwume kenaka nkuyisunga malo abwino.

Follow us on Twitter:

Ahttps://twitter.com/Malawi24

Advertisement