Tchimo kuzuza: Namadingo abisa botolo la mowa

Advertisement

Yemwe anayamba maimbidwe ngati oyimba nyimbo zauzimu Patience Namadingo, watekesa pa masamba anchezo kaamba ka kanema yemwe akumuonetsa akubisa botolo la mowa.

Kanema ina yomwe anthu akugawana pa masamba anchezo ikumuonetsa Namadingo ataima ndi mzake Cassim Ibrahim yemwe wayimba naye nyimbo ya ‘Sadziwa’ yomweso ambiri akuikonda.

Mukanemayi yomwe yajambulidwa awiriwa ataima pachinthu china chomwe chimazungulira, Ibrahim wanyamula tambula ya chakumwa chaukali, pomwe mbali inayi Namadingo wanyamula botolo lomwe ena akuti ndi la Castel Lite.

Katswiriyu yemwe anaimba nyimbo ya ‘Mtendere’, wazizwitsa anthu ndi ukadaulo omwe waonetsa mukanemayi pomwe amabisa botolo la mowa lomwe ananyamula kuti lisaoneke.

Namadingo amati chinthu chomwe awiriwa anaimapo chikamazungulira, amathawitsira botolo la Castle Lite kumbuyo kwa Ibrahim ndi cholinga choti lisaoneke.

Komabe ntchito yobisa botolori siyinaphule kanthu kaamba koti kangapo konse linawoneka zomwe zapangitsa kuti kanema yawoyi ikhale yachikoka pa masamba anchezo.

Munthu wina pa thwita wati wadabwa kuti oyimbayi akudzizuzilanji ndikubisa mowa pomwe atha kuchita zomwe akufuna kaamba koti ananena kale kuti iye siwoyimba nyimbo zauzimu.

“Ndalama ndizako nde chobisila botolo la mowa ndi chiyani? Ingovomelezani kuti mumamwa mowa basi osati kudzivutitsa chonchi, komaso paja munatiuza kale kuti iwe siiwe oyimba wa gospel,” watelo munthu wina pa thwita.

Munthu winaso patsamba lina pa fesibuku, wati: “Zobisa mowazo ndezichani??? mesa tonse timadziwa kut umamwa mowa?”

M’chaka cha 2020, Namadingo anadabwitsa anthu pomwe anabwera poyera mkunena kuti anthu omwe akufuna oyimba wa bwino yemwe amatchula za Yesu komanso Mulungu munyimbo iliyonse ayang’ane kwina.

“Kwanthawi yomaliza yankho n’lakuti ayi, sindine woyimba nyimbo zauzimu, ndine woyimba chabe, ndi ntchito yanga, ndikukhulupirira kuti nanunso muli ndi ntchito ndipo palibe ntchito zauzimu, ndimasankha zoti ndiyimbe,” anatelo Namadingo mu 2020.

Follow us on Twitter:

Advertisement