Ogwira ntchito ku khonsolo ya Balaka akwiya ndi kuchedwa kwa malipiro

Advertisement

Ogwira ntchito mu nthambi zosiyanasiyana za boma ku khonsolo ya Balaka mam’mawa uno akhamukira ku ofesi za Khonsolo ya bomali ati kamba ka kusakondwa ndi kuchedwa kwa malipiro a mwezi wa May.

Ogwira ntchitowa ati akufunanso mayankho kuchokera kwa akuluakulu a khonsoloyi pa chomwe chimachititsa kuti nthawi zonse azichedwa kulandira malipiro awo a pamwezi.

M’modzi mwa anthu ogwira ntchitowa a Patricia Chimwala adandaula kunena kuti kuchedwa kwa malipiro kwawakhudza kwambiri kamba kakuti akulephera kupeza zinthu zofunikira za tsiku ndi tsiku.

Pakadali pano, oyimira ogwira ntchitowa ali ku kachipinda komata komwe akukambirana ndi bwanamkubwa wa bomali a Darwin Mngoli komanso akuluakulu ena apa khonsoloyi.

Follow us on Twitter:

Advertisement