Oyimba hipapu ambiri akumveka ngati Gwamba – watero Dominant 1

Advertisement

…wati nyimbo zambiri ku Malawi ndi mbwelera

Oyimba nyimbo zogwira palisani, hipapu (hiphop), Dominant 1 wabweretsa chifwilimbwiti pa masamba amchezo pomwe wang’alura oyimba anzake kuti ambiri akubera mmene amaimbira Gwamba ndipo wati nyimbo zambiri ku mpanje kuno ndi panja penipeni.

Nkhaniyi yayamba kumayambiliro kwa sabata yatha pomwe Dominant 1 yemwe pano a kukhala m’dziko la South Africa analemba pa tsamba lake la fesibuku kuti oyimba hipapu ambiri ku Malawi kuno akuveka ngati Gwamba.

“Ndimamvera nyimbo za a Malawi pa intaneti, ambiri mwainu mukuveka ngati Gwamba. Tsopano chimenecho nde chikoka,” watelo Dominant 1 muwuthenga omwe anaulemba mchizungu.

Uthengawu wakwiyitsa oyimba ambiri a chamba cha hipapu komaso anthu okonda chambachi omwe pano akumuponya miyala oyimba mzawoyu yemwe pena amadziwika ndi dzina loti D1.

Ambiri mwa anthu omwe akumusambitsa chokweza, ati D1 anatha ndipo ena monyogodola ati sakumudziwa mkomwe oyimbayu yemwe m’mbuyomu wawinapo mphoto zosiyanasiyana pa mayimbidwe.

“Dominant 1 anthu akufunsa kuti chifukwa chani Munachoka Ku Malawi Muli Legend ndikupita Ku South Africa kukakhala Upcoming Artist? (oyimba oyamba kumene)” wafusa munthu wina pa fesibuku.

Mawu oti anatha akwiyitsa D1 yemwe lachinayi m’sabata yomwe ikungothayi wazijambula kanema yomwe anthu akugawana mmasamba anchezo yomwe wang’alura onse omwe akumunena kuti anatha.

Munkanemayi, Dominant 1 wati oyimba hipapu ambiri omwe akumunena kuti anatha mdziko muno, ndi ana osapola pamchombo omwe akuti abadwa muzaka za ma 2000, nthawi yomwe iye anali atatopa ndikuimba.

Apa iye anayikira kumbuyo zomwe wakhala akupanga Jolly Bro, pong’alura oyimba angapo m’dziko muno, ponena kuti ambiri ndiogunata omwe akuyenera kuphuzitsidwa zambiri.

“Anthu akamafusa unaimba nyimbo yanji, ndimangodziwa kuti unabadwa 2000, momwe umayamwa ine mnali nditadziwika kale, kupusa eti, munakanunkha mkodzo

“Nzosadawitsa kuti JB amakukalipilani tsiku ndi tsiku, zikomo Jolly bro, anthu awa samazitsata, upitilize kuwaphuzitsa zinthu,” anatero D1.

Pa nkhani ya Gwamba, D1 mu kanemayi anati anamudziwa kalekale ndipo wati amamulemekeza chifukwa choti amatha kuimba komaso poti ubale wawo unayamba kalekale.

D1 wasambwadzaso anthu omwe akumuseka kuti ali ndiomutsatira ochepa pa fesibuku ponena kuti zokhala ndiokutsatira ambiri pa masamba anchezo nzopanda phindu.

Apa anati oyimba kapena anthu otchuka ambiri m’dziko muno angokhala chabe ndi anthu owatsatira mmasamba anchezo pamene ndalama alibiletu ndipo wati kukhala ndi omutsatira ochepa pa fesibuku sikumakhudza mayimbidwe ake.

“Sindimasamala kutsatidwa ndi anthu ambiri kapena ayi chifukwa ine ndinayamba kuimba izi za masamba anchezozi kulibe. Chabwino sandutsani okutsataniwo zikhale ndalama. Kodi okutsataniwo amakudyetsani?” Wadabwa D1.

Iye walangiza oyimba aku Malawi kuti ayambe kuimba nyimbo zabwino, ponena kuti nthawi zambiri akabwera kuno kumudzi, nyimbo zomwe amadzazimva zimakhala phala lenileni.

“Tiyeni tipange nyimbo zambino, sinditchula mayina kuti uyu akuyimba nyimbo za bwino kapena ayi koma ndingoti tiyeni tiyimbe nyimbo zabwino. Nyimbo zambiri zomwe ndimadzaziva ndikabwera (ku Malawi) ndi nyasi, nyasi, nyasi. Mutha kundida mmene mungathere, komabe ndi nyasi,” wateroso D1.

Advertisement