Mabwalo amilandu ayimitsa ntchito zawo ku Zomba chifukwa cha vuto la madzi

Advertisement

Pamene vuto lakuvuta kwa madzi lafika tsiku lachisanu mu mzinda wa Zomba, mabwalo amilandu ayamba ayimitsa ntchito zawo tsopano.

Malawi24 itakayendera Bwalo la Chief Resident Magistrate komanso Bwalo lalikulu la Zomba High Court tidapeza ntchito zoweruza milandu zitayimitsidwa.

Izi zapangitsa kuti anthu omwe adatsekeredwa poganidziridwa kuti apalamula milandu yawupandu ndipo akuyembekezera kuti akawonekere kubwalo lamilandu akhalabe m’manja mwa a polisi mpaka madzi adzayambe kutuluka.

Bungwe la Southern Region Water Board lidayimitsa ntchito zake zopereka madzi mu mzinda wa Zomba sabata yatha Lachisanu potsatira kubedwa kwa zipangizo za bungweli.

Pakali pano Bungwe la SRWB likusoweka ndalama zokwanira 500 million kwacha kuti limangire malo omwe anthu okuba adaba zipangizowo.

Follow us on Twitter:

Advertisement