Zomavala mabamushoti, kumadikula, timiyendo ngati machesi, zithe – wabweza moto JB

Advertisement

…wati Lulu ndi Tay Grin ndi ‘mingochana’, anaba ndalama zothandizira ovutika ndi namondwe

…akuti dolo ndi Namadingo

Mamuna mzako mpachulu; kwavuta ndipo kwatelera, awawa apwetekana. Oyimba Jolly Bro wasambula Lulu pomunena kuti ali ndi timiyendo ngati machesi, anaba ndalama, komanso wati ndi “mngochana”.

Nkhaniyi ikutsatira zomwe anayankhula Lulu posachedwapa pomwe anati samamudziwa oyimba Hip Hop Jolly Bro yemwe amatchuka ndi dzana loti JB ndipo pano akukhalira mdziko la America.

Izi zinakwiyitsa JB yemwe lachisanu anaitanitsa likukumwe la anthu ku tsamba lake la fesibuku komwe wamuvulira Lulu yemwe posachedwapa anali mdziko la American komwe amakaimba.

Mkuluyu anayamba ndikumudzudzula Lulu kamba kogwirizana ndi Tay Grin. Iye wati oyinbawa analandira ndalama zomwe zinapezedwa pa maimbidwe omwe anapangitsa ku US zomwe akuti zimaenera kuthandizira anthu omwe anakhudzidwa ndi namondwe wa Freddy kuno kumpanje.

Pang’ono ndi pang’ono JB anayamba kulowa mkati ndi kuyamba kumusambitsa Lulu chokweza pomunena kuti anaguga ndipo nyimbo zake za kwasakwasa palibe amene amamvera.

Iye anati Lulu ndi munthu wa mkulu ndipo asiye zomavala timakabudula ting’onoting’ono ponena kuti zimamusambula kaamba koti miyendo yake ndi ing’onoing’ono ngati zotokosera m’mano.

“Masiku anowa ndindani amene amamvera nyimbo za munthu ovala kabudula kumadikula, kwasakwasa? Palibetu. Izi zomavala mabamushoti, gitala m’manja munthu wankulu kumadikula, timiyendo ngati ma toothpick (zotokosera m’mano) timiyendo ngati machesi, sizabwino.

“Nde munthu ukamazitenga ngati dolo otha kuimba kuposa amzako mpaka mkumati JB sindikumudziwa, umaona ngati zilibe zotsatira zake? Ukuona ngati anthu sadana nawe?” anatelo JB.

Ngati mwano umenewo siunakwane, JB anapitilira kulavula zakukhosi pomutchula Lulu kuti “Mngochana” chichewa chomwe munkuyankhula kwake chikutanthauza kuti anthu ogonana amuna kapena akazi okhaokha.

Iye anati anthu ogonana amuna kapena akazi okhaokha alipo ambiri mdziko muno koma wauza aMalawi kuti asalore kuti mwikho umenewu usefukire kuno ku Malawi.

“Zithunzi zayamba kutuluka apapa za anyamata otiwa tsitsi. Anthu awa ndikagulu, apapa nde kuti amuimbira Sibusiso wa ku Joni uja, homo uja, mwankumbukira? Kunoso ma homo ndiomwe ali m’ma high places, komano ku Malawi tisalore zimenezo, tisalore ka mngochana kena kake ka gitala m’manja, kavala kabudula, miyendo ngati toothpick, kazibwera apa kumadikula thimbwiza thimbwiza,” anaonjezera choncho JB.

Oyimbayu wayamikira Patience Namadingo kaamba kothandiza ndi ndalama oyimba mzake Lawi pomwe anali phwando la maimbidwe posachedwapa zomwe akuti Lulu sangapange ponena kuti alibe mtima othandiza amzake.

“Kuyambira leroli, Namadingo uja ndiye dolo. Anatenga ndalama zake za mthumba kumuthandiza Lawi, tikufuna anthu ngati amenewo, osati izi zovala kabudula mkumadikura. Munamuona Namadingo amapanga zimene zija? Namadingo nde dolo,” watelo JB.

Iye anabwereza kunena kuti Lulu pomwe anali ku South Bend amagona pa balaza ndipo anati zinthu zinasintha kaamba koti iye anaulura za nkhaniyi pa tsamba la nchezo.

JB anamaliza ndikuuza anthu kuti amukhulukire Lulu pa zomwe anayankhula komaso walangiza anthu kuti azipanga sapoti oyimba achimuna enieni osati Lulu ndi Tay Grin

“Awawa akhululukireni. Mngochana Lulu, mngochana Grin atayeni ndi ana awa. Pezani amuna enieni. Lulu ndi Tay Grin siowasankha kuti akaimilire magaye. Pezani amuna eni eni owapanga sapoti. Nanga mamuna amaziphoda?” anamaliza choncho JB.

Pakadali pano Lulu yemwe ndi Lawrence Khisa sanayankhe pa zomwe wayankhula Jolly Bro yemwe dzina lake lenileni ndi Alberto Fernando Zacarias.

Follow us on Twitter:

Advertisement