Bambo waletsedwa kupeleka umuna atabeleka ana 600

Advertisement

Zina ukamva ndithudi kamba anga mwala. Bwalo lamilandu ku Netherlands lalamula bambo wina wa zaka 41 yemwe akumuganizira kuti anabeleka ana pafupifupi 600 padziko lonse lapansi kudzera mukupereka umuna kuti asiye kupereka.

Malingana ndi malipoti a BBC, bamboyo yemwe akudziwika kuti Jonathan akuti adayamba kupereka umuna wake kuzipatala zobelekera za mdziko la Netherlands kuyambira m’chaka cha 2007.

M’chaka cha 2017, a Jonathan adaletsedwa kupereka umuna wawo ku zipatala zoberekera mdzikolo zitadziwika kuti anali ndi ana opitilira 100 zomwe ndikutsutsana ndi malamulo adzikolo.

Malamulo azachipatala mdziko la Netherlands samalora mamuna opeleka umuna kubereka ana osapitilira makumi awiri ndi mphambu zisanu (25) m’mabanja khumi ndi awiri (12).

Komabe, mkuluyu akuti adaphwanya malamulowa ndipo mmalo mwake anayamba kumapeleka umuna kunja kwa dziko la Netherlands komanso pa intaneti.

A Jonathan akuwaganizira kuti amabereka ana ena oposa 400 kunja kwa dziko la Netherlands, ndipo akukhulupirira kuti mkuluyu anathandiza kubereka ana pakati pa 550 ndi 600 pa dziko lonse la pansi.

Potsatira kuphwanyidwa kwa malamulowa, oweruza milandu ku Hague a Thera Hesselink, alamula kuti mkuluyu asiye kupeleka umuna wake kunja kwa dziko la Netherlands.

 Jonathan walamulidwaso kuti apereke mndandanda wa zipatala zonse komwe adapeleka umuna wake ndipo zipatalazo zalamulidwaso kuti ziwononge umuna wa mkuluyu omwe unali usanagwilitsidwe ntchito.

Bwaloli lati ngati a Jonathan anganyalanyaze chigamulochi, adzalipitsidwa chindapusa cha ndalama zokwana €100,000 zomwe ndi pafupifupi K150 miliyoni.

Follow us on Twitter:

Advertisement