Awilo watokosola aMalawi podya ndalama ya Lawi

Advertisement

Oyimba wa mdziko la DRC Awilo Longomba washosha mavu nkhomola kaamba kodya ndalama ya oyimba wa ku Malawi Lawi.  Awilo ankati abwera kudzaimba koma sanabwere ndipo pano sakuyankha foni.

Kuyambira chaka chatha, oyimba Francis Chris Phiri yemwe amadziwika kwambiri kuti Lawi, wakhala akukozekera phwando la maimbidwe lomwe likuyenera kuchitika lero ku Bingu International Conference Center mumzinda wa Lilongwe litalepheleka chaka chatha.

Ngati njira imodzi yowonetsetsa kuti phwandoli lidzakhale lapamwamba komaso la chikoka, Lawi anaitana oyimba waku DRC yemwe pano a kukhala ku UK Awilo Longomba kuti adzaipatse moto patsikuli.

Huuu! Mphuno salota, oyimbayu yemwe amaimba chamba chovinika cha soukous, sanabwere mdziko muno ndipo zadziwika kuti ndalama K15 miliyoni yomwe Lawi anamutumizira oyimbayu kuti abwere kuno yalowa m’madzi.

Malingana ndi Lawi, Awilo anatumizilidwa ndalama ina chaka chatha koma sanabwere ndipo chaka chino anapatsidwaso ndalama ina ya malipilo komaso ya mayendedwe ndipo amayenera kufika mdziko muno lachitatu.

Komatu Awilo tikuyankhula pano sanafikebe mdziko muno ndipo malipoti akusonyeza kuti ali mdziko la Nigeria komwe akupanga za maimbidwe a achinyamata ndipo akaimbilidwa foni sakuyankha.

“Ineyo ndisabise, ndine okwiya kwambiri. Kuyambira chaka chatha ndalama tinatumiza, tikawerengera zina ndi zina zikukwana pafupifupi K15 miliyoni. Ndine okwiya, titafufuza tapeza kuti anthuwa sanapite ndikomwe ku malo okwelera ndege.

“Pano nditafufuza ndapeza kuti ali ku Nigeria. Ndikaimba foni sakuyankha pamene amayenera akhale wakwera ndege yobwera kuno ku Malawi,” wadandaula Lawi.

Iye wati akuganiza kuti Awilo wapanga chipongwechi kaamba koti ndalama ina anapatsidwa chaka chatha pomwe phwando lamaimbidweli limayenera kuchitika mwezi wa Disembala koma silinachitike.

Nkhaniyi yakwiyitsa aMalawi ochuluka kuphatikizapo oyimba Lucius Banda yemwe walemba pa tsamba lake la Facebook kuti nayeso mmbuyomu anapangidwa chipongwechi ndi Awilo.

“Ifenso adatizuza titamulipira kale, anakana kukakwera ndege. Tidamutumizira adzukulu ku UK konko adakaikwera ndege asakufuna, adabwera. I may not be able to join Namadingo since i am commited in mchinji. Koma Na dollayo nde Abweza afune asafune. Malawi lets support our son tomorrow. My heart is with you “Angoni” Lawi,” watelo Banda.

Tikuyankhula pano aMalawi ochuluka akhamukira ku tsamba lanchezo la Facebook la Awilo komwe akumulavulira zakukhosi.

“Ndalama Lawi anachita kulima soya iwe sungangodya mophweka choncho ubwenze,” watelo munthu wina ku tsamba la Awilo.

Pakadali pano, oyimba otchuka Patience Namadingo wadzipeleka kuti akaimba kuphwandoli mwaulele ndipo wapepesa Lawi kaamba ka zomwe wakumana nazozi.

“Ndapanga chiganizo choti ndikuthandize. Ineyo ndikaimba nawo nthawi yokwanira ndithu. Ndinakakonda kuti naneso unakandipatsa ndalama komano ndi mmene zililimu ndikaimba ulele, usakandipatse ndalama.

“Pali nthawi zina tiziimba kuti tipange ndalama koma ino ndi nthawi yoimba kuti tithandizane chabe. Ndinakuuza kuti ndibwera kudzaonera koma pano ndibwera kudzaimba,” watelo Namadingo.

Follow us on Twitter:

Advertisement