‘Awa ndionama basi’: Makawa wang’alura asing’anga

Advertisement

Lolemba sabata ino, ‘Mbuyache Makawa’ monga momwe amadzitchulira munyimbo zake, watulutsa nyimbo ya tsopano yomwe akuitchula kuti ‘Bosh’ yomwe wajambula ndi Drue G pomwe kanema yake  yajambulidwa ndi Mega.

Mu nyimbo ya ‘Bosh’ yomwe tanthauzo lake ndi ‘Bodza’, Makawa akudzudzu makhalidwe omwe a sing’anga akuchita pomabera anthu ndalama pomawanamiza kuti ali ndi mtera osiyanasiyana.

Mu vesi yoyamba ya nyimboyi, Makawa yemwe anaimbaposo nyimbo ya ‘Kwathu Kwavuta’ yomweso imadzudzu mchitidwe wa ufiti, wati a sing’anga omwe amauza anthu kuti ali ndi mankhwala olemeretsa ndi a kathyali.

“Kodi wayala mankhwala apa mndani?                                     Wayika chikwangwani apa mndani? Ndindani?                    Waika nsalu apa mndani yolembedwa kuti dokota mwakuti?                                        Akuti ali ndi njoka ya thunga, nsenda wana, nkola ntchentche, Awa ndionama basi.                    Akuti muli ndi chikwama waleti, munthu alemere nsanga. Iwe osangotenga chikwama waleti ulemere wekha,” yatero ndime yoyamba ya nyimbo ya Makawa.

Makawa watiso a sing’anga ambiri a kukhala m’matauni osati kungofuna kubera anthu ndalama kokha komaso ena cholinga chawo nkufuna kuvula akazi a eni ake omwe amawapatsa zitsamba zonama.

Iye wati a sing’anga ambiri omwe akumaitanira anthu kuti ali ndi mankhwala olemeretsa komaso okulitsa chida cha a bambo ndi abodza ndipo anthu asamawakhulupilire.

“Ili ndi bodza, kuba uku, limeneli bodza.                                       Kwinaku akunama ali ndi nsenda wana.                                                                        Ndati ili ndi bodza, kuba uku, limeneli bodza.                                 Ati amakuza chida cha abambo, Ndati ili ndi bodza, kuba uku, limeneli bodza.                      Akumanama ali ndi chitaka waleti Ndati ili ndi bodza, kuba uku, limeneli bodza,” ikumatelo kolasi ya nyimbo ya Bosh.

Pakadali pano nyimboyi yomwe yaimbidwa muchamba cha makono cha amapiano, yalandilidwa ndi anthu moyisanasiyana komaso yadzetsa zoyankhula mmakwalalamu ndi m’masamba a nchezo.

Podziwa kuti mvula ikagwa kuchuluka zoliralira, anthu ena akuyamikira kuti nyimboyi yayimbidwa bwino komaso kanema wake ndiopatsa chikoka, pomwe anthu ena akuti nyimboyi ndi panja penipeni.

“Naye Mbuyache Moses Makawa sakulora. Nyimbo zake zausing’anga zija wazilowesa ku Amapiano naye asasalire m’mbuyo.  Komanso mbuyache nde wasamba eh eh mpakana kumavina ndi akazi amenewo ayi zikomo,” layamikira choncho tsamba lina pa Facebook.

Mbali inayi, ka nunsu ka anthu ena makamaka m’masamba a mchezo, kati nyimboyi inakakhala yokoma kwambiri Mbuyache Makawa anakayiyimba muchamba cha lokolo chomwe amadziwika nacho osati amapiano.

“I have listened to a new music for Moses Makawa Titled Bosh (ndamvera nyimbo ya tsopano ya Moses Makawa mutha wake Bosh). Bosh ati akutathauza kuti Bodza, Moses Makawa anasiya kuimba chifukwa chama busy ndi ntchito. Makawa he is a teacher by profession (Makawa ndi phunzitsi).

“Koma ineyo nyimboyi sikusangalasa chifukwa ikusowa the energy which Moses Makawa anali nayo ndi yomwe timamamudziwira,” wateloso munthu wina pa Facebook.

Moses Makawa yemwe amachokera m’mudzi mwa Mkuta mfumu yayikulu Mabuka m’boma la Mulanje, watulutsa nyimbo ya Bosh patatha zaka zoposera zisanu chitulutsileni nyimbo zina.

Zina mwa nyimbo zomwe Mbuyache anatchuka nazo kwambi ndi monga; Khuzumule, Ali Manjamanja, Lithe, Mubwera Liti, Mfiti Ulemu kungotchulapo zochepa chabe.

Follow us on Twitter:

Advertisement