Si ine – mlimi ofusa Chakwera wakana kuti wapandidwa

Advertisement

Zakaliya (Kumanja) kuyankhula ndi a Chakwera

Mlimi wa fodya yemwe anafusa mtsogoleri wadziko lino Lazarus Chakwera fuso lothina, wakana kuti wamenyedwa ndi apolisi.

Izi zikutsatira makanema awiri amene anthu akugawana mmasamba anchezo omwe anajambulidwa lero pomwe mtsogoleri wadziko lino amakatsekulira malonda afodya mumzinda wa Lilongwe.

Kanema oyamba akusonyeza mlimiyu Msaiwale Zakaliya wina akuyankhulana ndi a Chakwera ndipo anafusa mtsogoleri wa dzikoyu kuti mchifukwa chiyani mitengo ya mbewu zina yakwera kwambiri kuyerekeza ndi mtengo wa fodya chaka chino.

“Chimanga chachoka pa K220 pa kilo kufika pa K500, soya wachoka pa K380 pa kilo kufika K800. Nde ndimadabwa kuti anzathu awaonjezera ndi K300 ena K200 koma ife a fodya mwationjezera ndi K50, tidalakwanji kufodya kuno,” anadandaula choncho mlimiyo.

Mbali inayi kanema wachiwiri akusonyeza mkulu wina akugwiridwagwiridwa ndi apolisi ochulukirapo ndipo anthu ena anayamba kufalitsa kuti ogwiridwagwiridwayo anali mlimi odandaulayo.

Koma patangodutsa maola ochepa mlimi yemwe anayankhula ndi a Chakwera yemwe wazindikilidwa ngati Msayiwale Zakaliya wabwera poyera ndikutsutsa mwantu wa galu kuti iye wapandwa.

“Ine ndi Msaiwale amene ndinayankhulana ndi pulezidenti Chakwera lero. Zimene anthu akufalitsa pa sosho midiya (social media) kuti ndamenyedwa, ayi ndithu ndili bwino bwino monga umo mundioneramu.

“Limenelo ndi bodza sindikudziwa kuti zimenezo akuzitenga kuti, ine ndili bwino bwino. Ndilibe vuto lili lonse, palibe wandimenya, palibe wandigwiragwira mthupi, ndi sefu (safe), ndili kilini (clean), limenelo ndi bodza,” watelo Zakaliya.

Pakadali pano mneneri wa apolisi mdziko muno a Peter Kalaya wazindikira mkulu amene kanema yake ikuonetsa akugwiridwagwiridwa ndi apolisi ngati a Dala Kadula omwe ndi kafa nikhale wa chipani cha MCP.

Malipoti akusonyeza kuti akuluakulu a mwambowu anakhazikitsa lamulo loti achipani cha MCP asalowe ndipo anapita kwa apolisi omwe amaletsawo mkuyamba kukangana nawo kuti azimai achipani cha MCP alowe.

Tikukamba pano, naye Kadula watulutsa kanema yake yomwe anthu akugawanaso m’masamba a mchezo yomwe akufotokoza momwe zinakhalira kuti afike pogwiridwagwiridwa ndi apolisi.

Mkati mwa kanemayi Kadula wati iye monga mwa nthawi zonse samamenyedwa komaso samachitidwa kanthu kali kose koma wati iye ngati mtsogoleri wa a “nyani” lero anapita pa galaundi kuti akagwire ntchito take.

Iye wati anali odabwa kuti “apolisi amaletsa otsatira chipani chomwe chikulamura boma pano kuti asalowe mkati mu.”

Follow us on Twitter:

Advertisement