Osatitchula zidakwa, mowa timamwela kusangalala basi – watero mbiyang’ambe Dausi

Advertisement

…boma likupanga malamulo atsopano okhaulitsa ma dalaiva a chakumwa

Phungu wa dera la pakati mu boma la Mwanza a Nicolas Dausi anachemetsa ku nyumba ya malamulo pamene anadzudzula nduna ya boma kuti imanyogodola anthu omwa mowa kuwatchula kuti ndi zidakwa. A Dausi anati iwo monga mkulu wa chakumwa, mawu awa sanawakhalire bwino.

Mdando wa a Dausi unabwera pamene a boma analengeza kuti akufuna kukhazikitsa malamulo a tsopano ofuna kukhaulitsa anthu onse okonda chakumwa komanso kuyendetsa galimoto kabanga ali mmutu.

Malinga ndi nduna yoona za m’dziko a Ken Zikhale Ng’oma komanso anzawo owona za mayendedwe a Jacob Hara, boma likufuna kukhazikitsa malamulo a tsopano ofuna kuthana ndi mchitidwe oyaka ndi kumakayenda ndi galimoto.

A Ng’oma ananena kuti anthu okonda chakumwa kuno ku Malawi, ngati sakufuna kulumidwa ndi lamulo, azitengana ndi anzawo osamwa mowa kuti aziwayendetsa. Iwo mu kufotokoza kwawo anagwiritsa ntchito mawu oti zidakwa, zimene zinawayipira a Dausi.

Poima pa ndondomeko yofuna kukonza kalankhulidwe ka mu nyumba ya malamulo, a Dausi ananena kuti a Zikhale agwiritsa ntchito mawu olakwika ofotokoza anthu omwa mowa.

“Anthu enafe mowa timamwera kusangalara, ena amamwera kuti ayiwale mavuto, si zoona kutitchula kuti zidakwa,” phunguyo anatero, zimene wachiwiri kwa sipika wa nyumba ya malamulo anagwirizana nazo ndi kupempha a Zikhale kuti akonze kafotokozedwe kawo.