Awa apwetekana; abusa a Blantyre sinodi akufuna kulodzana, kugwebana yamanja

Advertisement

Zamasiku otsiliza. Abusa awiri ampingo wa CCAP, sinodi ya Blantyre, apindirana ndebvu mkamwa uku, ndipo akuti kaya nkulodzana alodzana ngakhaleso ndewu yamanja apambadzana, akuti sakuopana.

Chinkanganochi chili pakati pa abusa awiri omwe alavulirana za mkamwa pa lamya ya mmanja yomwe awiriwa anaimbirana sabata yatha.

Malingana ndi kilipi (audio clip) ya zomwe awiriwa amayankhulana yomwe tsamba lino lapeza, mkanganowu ukuoneka kuti wadza kaamba ka zisankho zomwe sinodi ya Blantyre ikufuna kupangitsa posachedwapa.

Mukukangana kwawo, abusa ena akuloza chala abusa anzawo kuti akumachita miseche komaso ukazitape ndicholinga choti m’busa winanso wa mpingowu adzawine pa udindo wa ulembi wa sinodiyi pa zisankho zomwe zichitike mkati mwa chakachi.

Abusa oyambawawo omwe amamveka okwiya zedi, awopseza kuti alowa pa galaundi ndipo anenetsa kuti abusa achiwiriwa komanso anzawo ena sangamugwedeze kumbali yolodzana muufiti komaso kumbali ya zigogodo.

“Inuyo zomwe mukupanganazo ineyo ndikulowano pa galaundi. Ndipanga zainu, Achimwene ineyo ndikhoza kukumenyani pamanja komanso olo paufiti ndikhoza kukumenyani.

“Ngati ili ndewu nditha kubwera pakhomo panu mawa kuti ndimenyane nanu. Ineyo ndatopa, ndatopa nanu alomwe zitsilu zachabechabe. Iweyo ndi nzako muwuzane, ine zopusa ndimakana,” m’busa woyambayo watero.

M’busa woyambayu wadandaulaso kuti abusa enawa akhala akufalitsa nkhani zochuluka zoyipitsa mbiri yawo kuphatikizapo kuwanamizira kuti anapeleka mimba kwa mtsikana wina mu mpingo wawo.

Iwo atiso abusa anzawo ochuluka ku sinodiko akuwadanitsana.

M’busa woyambayu amayankhula mobwerezabwereza ndi motsindika kuti abusa ena awiriwo ndi
makanda kwa iwo pankhani ya mankhwala azitsamba komanso pankhani ya zigogodo.

“Achimwene ineyo sindimakuopani. Olo itakhala ndewu yamanja simungawine olo atakhala mankhwala inuyo ndi anzanuwo simungawineso,” anateloso m’busa Mulowa.

Mbali inayi mbusa wachiwiriyi yemwe amamveka odekha, sanayankhule zambiri koma mkati mwakuyankhulana, anati anamvadi zoti m’busa mzawoyo amapangadi za mankhwala achikuda.

“Nzowonadi anthu amakamba kuti inuyo mumapangadi zimenezo koma ineyo sindimapanga zimenezo. Za ndewu mwanena kwambiri, koma ine sindikupanga ndewu ndiinu, inu ndamene mukufuna muzandimenye nde bwerani muzandimenye,” anatelo abusa achiwiriwo.

Iwo anawauza woyambawo kuti anakakhala ofuna kuwapanga chipongwe anakawapanga kalekale ndiposo anakana kuti sakanena kwa m’busa nzawo zomwe amatumidwa zonyozazo.

Komatu kumapeto kwa foniyo m’busa wachiwiriyo anayamba kubweza moto ndipo anamuuza m’busa mzawoyo kuti nawo samamuwopa.

“Mwatsoka foni yanga ithima pompano koma ikamathima foniyi musaone ngati ineyo ndikukuopani, ndimafuna ndivetsere zonse mwayankhulazi,” anateloso m’busayo.

Kilipiyi ikusonyeza kuti abusa achiwiriwa ndi amene amatepa zokambiranazo kaamba koti foniyi itadulidwa, mkazi wawo anamveka chapasipasi akuwadandaulira amunawowo kuti anawauza kale kuti asamapange nawo zimenezo.

Pakadali pano, akuluakulu a sinodiyi sanabwere poyera ndikuyankhulapo za mkanganowu omwe ena m’masamba a nchezo ati uli ndikuthekera kobalalitsa akhilisitu a mpingowu ku sinodi ya Blantyre.

Advertisement