Senior Chief Malemia yathokoza chifukwa chowakwezera mafumu malipiro

Advertisement

Senior Chief Malemia ya boma la Zomba yathokoza boma chifukwa chokwezera mafumu malipiro ndipo ati izi zipangitsa kuti mafumu azilimbikira ntchito.

Senior Chief Malemia yawuza Malawi24 kuti mafumu andodo a Boma la Zomba akondwera kwambiri chifukwa poyamba amalandira swahala wochepa kwambiri.

Iwo ati mafumu amagwira ntchito yotamandika kwambiri m’madera momwe amakhala choncho kukwezeredwa swahala kupangitsa kuti mamfumu adzilimbikira ntchito yawo. Koma pamenepa Senior Chief Malemia adapempha boma kuti ngakhale kuti awonjezera kawiri swahala wawo ndikofunikanso kuti awaganizire mamfumu ang’ono ang’ono chifukwa ndalama yomwe amalandira ndiyochepa kwambiri kuyelekeza ndi ntchito yomwe amagwira.

Iwo ati mafumu amakhala ndi udindo waukulu m’makomo mwao ndipo alinso ndi ana omwe amafuna akumawatumiza sukulu zapamwamba koma amalephera chifukwa choti amalandira ndalama yochepa.

“Mafumu ang’ono ang’ono amalephera kugula thumba la fetereza chifukwa choti ndalama yomwe amalandira ndiyochepa choncho ndipemphe boma kuti nawonso awaganizire powakwezera mswahala kuti adzitha kugula fetereza,” adatero Senior Chief Malemia.

Senior Chief Malemia yalangizanso mabanja achifumu kuti asalowetse mikangano ya ufumu pamene Boma lakweza malipiro amafumu.

Iwo ati pamene boma lakweza malipiro chonchi sikuti akwezera mafumu omwe akutsogolera pakali pano ayi koma aliyense olowa ufumu wina akamwalira adzidzalandiranso chimodzimodzi.

Boma lakweza malipiro amafumu kawiri ndi ndalama yomwe adali kulandira poyamba ndipo akatswiri owona zaulamuliro wabwino ati zomwe lachita boma pokweza malipirowo zipangitsa kuti mafumu azigwira ntchito yawo mokhulupilika komanso mopanda kuchita zachinyengo.

Poyamba ma Sub T/A adali kulandira K18,000 koma tsopano azilandira K36,000, ma Senior Chief amalandira K60,000 koma tsopano adzilandira K120,000 ndipo ma Paramount Chief amalandira K100,000 ndipo tsopano azilandira K200,000 kwacha pa mwezi.

Follow us on Twitter:

Advertisement