Atipweteka, atisenda ndipo atiyalutsa: Ijipiti ya Mo Salah 4 Malawi ya Marinica 0

Advertisement

Zoti tiri pa chisoni sizinaoneke. Zoti tate wathu ndi m’busa sizinaonekenso. Pena kumati mwina malaya ofiyira tinavala lero anamusokoneza mmaso Mo Salah kuti amayesa ndi Manchester United. Chifukwa atiswa ndipo atisambitsa chokweza. Olo naye kochi Mario Marinica wayenda wa uyo uyo pochoka pa Bingu. Zamanyazi zenizeni.

Timu ya mpira wa miyendo ya dziko lino lero yaudziwa mpira pamene yaumbudzidwa ndi timu ya dziko la Ijipiti. Pa masewero amene anachitikira mu mzinda wa Lilongwe pa bwalo la Bingu stadium, zinaonekelatu kuti mu dziko muno cha mpira mulibemo.

Malodza anafikiridwa kumayambiliro komwe pamene timu ya Egypt inamwetsa chigoli mu mphindi yachinayi. Anali mnyamata Tarek Hamed amene anapereka uthenga oti lero palibe kudyera nyama pa Bingu.

Patangotha mphindi zongoposera khumi ndi mphambu ziwiri, timu ya Ijipiti inaonetsetsa kuti ikhaulitse Malawi pa kwawo pomwe poonjezerapo chigoli china. Mnyamata Omar Marmoush ndiye anaonjezerapo chigoli china kupangitsa kuti ikhale 2 kwa chilowere.

Nthawi imene mwina dziko lonse limayembekezera sinachedwe kukwana. Patangotha mphindi zinayi Malawi itakhomedwa msomali wachiwiri, katswiri wa timu ya ku mangalande ya Liverpool, Mohammed Salah, anadyetsa njomba kenako ndikukaumalizira mpira mu ukonde.

Pamene nthawi imati ma minitsi 20 ndiye kuti anthu atavomereza kale kuti Flames lero ndi maliro ena, palibe chimene chingatoredwe. Anthu amene anali mu Bingu ndi kuti pompo anasintha timu yokwera ndi kusanduka aiguputo.

Mu mphindi 25 zotsala kuti chigawo choyamba chithe, timu ya dziko lino inayesetsa kuteteza ndipo Ijipiti sinagoletse china. Popita kukapumulira, ndiye kuti zigoli zili zitatu kwa du, osewera a Flames asakuonetsa konse makani. Kungonyowa ngati kapinga wa pa Bingu National Stadium amene anavumbidwa mpira usanayambe.

Ngati Mo Salah amayesa kuti Malawi ndi Man United chifukwa cha zovala zofiira, zikuoneka kuti kokapumira anamukumbutsa kuti iyi chabe ndi Malawi ndipo idakali pa maliro a Freddy.

Mu chigawo chachiwiri, anyamata a Ijipiti anangochinya chigoli chimodzi chokha basi. Ahmed Sayed anamwetsa patangotha mphindi zisanu mpira chiyambireni. Ichinso chinali chigoli chomaliza cha mpirawu.

Anakhumudwa anthu okonda Malawi ndipo mpira usanathe anayamba kuponya ma botolo mu bwalo la masewero.

Advertisement