Ophunzira a Sukulu ya sekondale ya Balaka achoka pasukulu

Advertisement

Ophunzira pa sukulu ya sekondale yogonera konko ya Balaka achoka pa sukulupa ndipo ena afika kale m’makwawo ati kaamba ka kusakhutitsidwa ndi zakudya zomwe amapatsidwa pasukuluyi.

Malawi24 yamvetsedwa kuti ana ena afika m’makwawo m’bandakucha wa tsiku lalero lamulungu.

Poyankhula ndi Mtolankhani wathu, ophunzira ena amene tinawapeza akungozungulira mu tawuni ya Balaka ati atopa  ndi kudya zakudya zosakhala bwino kwa nthawi yaitali ngakhale adapeleka madandaulo awo kwa oyang’anira sukuluyi.

”Taganiza kuti tichoke ndipo tizabwelera pa sukulupa oyang’anira sukuluyi akazakonza vutoli,” Iwo adatero.

Padakali pano, oyang’anira sukuluyi ali pa mkumano wadzidzidzi limodzi ndi akuluakulu oyang’anira sukulu mchigawo cha maphunziro ku dera lakummwera Cha kummawa(SEED).

Follow us on Twitter:

Advertisement

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.