Namondwe wapita koma mvula ya mphamvu igwabe m’madera ena — yetelo MET

Advertisement

Nthambi yoona zanyengo ndi kusintha kwa nyengo yati namondwe wa Freddy yemwe wasakaza madera ambiri maka mchigawo chakumwera, wapita koma mvula ya mphamvu ipitilirabe kugwa m’madera ena.

Izi ndi malingana chikalata cha chidziwitso chomwe Nthambi Yoona Zanyengo ndi Kusintha kwa Nyengo yatulutsa lero lachinayi pa 16 March.

Munchikalatachi nthambiyi ya MET yati namondwe wa Freddy watha dzulo lachitatu pa 15 March ndipo yati chidziwitsocho ndichomaliza pankhani zokhudza namondweyo.

Ngakhale zili choncho, nthambiyi yati m’madera ochuluka mdziko muno apitilirabe kulandira mvula yomwe akuti itha kukhala ya mphavu kwambiri makamaka madera ambiri amphepete mwa nyanja.

Nthambiyi yati mvula yamphavu yomwe ingagweyi ndi kamba ka mpweya wachinyontho yomwe akuti ikuchokera mdziko la Congo zomwe akuti zitha kupangitsa kuti madera ena mukhale kusefukira kwa madzi.

“Ngakhale kuti namondweyu watha, madera ambiri am’dziko muno apitirirabe kulandira mvula yomwe igwe ya mphamvu m’madera ena makamaka m’madera amphepete mwa nyanja ya Malawi kamba ka mkumano wa mphepo otchedwa ITCZ mothandizana ndi mpweya wa chinyontho ochokera ku Congo.

“Chiopysezo cha kusefukira kwa madzi chikuyembekezeka kukhala chokwera makamaka m’madera amphepete mwa nyanja ya Malawi, choncho, tikhale tcheru,” yatelo nthambiyi.

Nthambiyi yatsimikizira a Malawi kutu ipitiriza kuunika mu Nyanja ya mchere ya India ndipo ngati Namondwe angabadwe winaso, idzadziwitsa mtundu wa a Malawi.

Pofika Lachiwiri, nthambi yowona za ngozi zogwa mwadzidzi yati, namondweyu yemwe anayambitsa kusefukira kwa madzi, mphepo yamkuntho ndi matope, zakhudza mabanja 19,676 (pafupifupi anthu 88,312) ndipo nthambiyi yati pakhazikitsidwa malo oyembekezera okwana 165, pomwe chiwerengero cha anthu omwe amwalira chafika pa 225, pomwe 707 ndiomwe avulala ndi 41 omwe asakupezekabe.

Follow us on Twitter:

Advertisement