Asilikali awiri apamadzi sakupezeka ku Mulanje

Advertisement

Asilikali awiri omwe amafuna kupulumutsa anthu ena omwe akhudzidwa ndi madzi osefukira m’boma la Mulanje, sakupezeka.

Malingana ndi nduna ya za ma boma a Richard Chimwendo Banda omwe ali pa Mkando m’boma la Mulanje, asilikali atatu a pamadzi ananyamuka pa bwato ndicholinga chofuna kukapulumutsa anthu ena omwe anali pamwamba pa malo othilira mafuta agalimoto.

Malipoti akusonyeza kuti asilikaliwa ali mkati mwa ulendo wawo, bwato lomwe anakwelaro linazima ndipo linayamba kukokoloka ndi madzi aphanvu omwe ali mdelari.

Bwatoli linakagunda mtengo zomwe zinapangitsa kuti litembenuzike ndipo munthu wamba mmodzi komaso asilikali awili ndi omwe anakwanitsa kuwolokera ku mtunda koma asilikali atatu anasowa.

Patatha ka nthawi kochepa, a Chimwendo Banda anauza anthu kuti msilikali mmodzi mwa atatu omwe anasowawa wapezeka ali mu mtengo wina.

Ndunayi yati pakadali pano ntchito ili mkati yosaka asilikali akusowawa ndipo ati pali chiyembekezo choti awapeza ali ndimoyo ponena kuti anavala zovala za pamadzi zomwe zimathandizira kuti munthu asamile.

Follow us on Twitter:

Advertisement

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.