ESCOM yakana kuti ikulumikiza magetsi mwaulere

Advertisement

Pamene anthu ena chimwemwe chinadzadza tsaya kuti nyumba zawo zilumikizidwa magetsi mwaulere, kampani yogulitsa mphamvu za magetsi ya Electricity Supply Corporation of Malawi (ESCOM) yatsutsa malipoti oti yayamba kulumikiza magetsi mwaulere kwa aMalawi.

Kumayambiliro kwa sabata ino, mphekesera zinali ponseponse kuti kampani ya ESCOM yayamba ntchito yolumikiza magetsi mwaulere kwa anthu pafupifupi 180,000 pansi pa ndondomeko ya Malawi Electricity Access Project (MEAP).

Kuphatikiza apo, nyumba zina zofalitsa mawu mdziko muno zinalengeza kuti ESCOM ikuyendetsa ndondomekoyi ndi ndalama zangongole zomwe inatenga ku Banki yaikulu padziko lonse ya World Bank zokwana 105 miliyoni dollars za m’dziko la America, zomwe ndi pafupifupi K105 biliyoni kuno kathu.

Koma poyankhapo pa mphekeserazi, kampani ya ESCOM kudzera mu chikalata chomwe yayulutsa lachiwiri pa 7 Malitchi, 2023, yati nkhaniyi ndi bodza la mkunkhuniza.

Kampani ya ESCOM yati kudzera mu ndondomeko ya MEAP, ikulumikiza magetsi kwa anthu amene analipira kale ndalama koma akhala nthawi yaitali asanalumikizilidwe magetsi ku nyumba zawo komaso kwa amene akulipira kumene.

“Sizowona kuti ESCOM yayamba kulumikiza magetsi mwaulere kwa aMalawi okwana 180,000 m’maboma onse a dziko lino monga m’mene ena akufalitsira.

“Zoona zake ndizakuti kudzera mu ndondomeko yotchedwa Malawi Electricity Access Project (MEAP), ESCOM ikulumikiza magetsi kwa anthu omwe analipila kale komanso amene akulipira tsopano kuti iwalumikizile magetsi. ESCOM ikugwira ntchitoyi pofuna kuchepetsa vuto la kuchedwa kwa ntchito yolumikiza magetsi chifukwa chakusowa kwazipangizo,” yatelo mbali ina ya chikalatachi.

Kampaniyi yatsindika ponena kuti  ntchitoyi ikukhudza anthu amene akwaniritsa ndondomeko zonse kuphatikizapo kulipira kale ndalama ndipo akungoyembekezela kuti ESCOM iwalumikizile magetsi ku nyumba zawo.

Malingana ndi chikalatachi, ndondomeko ya MEAP yomwe akuti inayamba mu 2022 ndipo ikuyembekezeka kutha chaka cha mawa, ikugwiridwa ndindalama zokwana 65 miliyoni dollar za mdziko la America zomwe akuti zinachokera ku World Bank.

Follow us on Twitter:

Advertisement