Tigwirane manja: Chakwera apempha maiko osauka kuti ayende limodzi ndi mtima umodzi

Advertisement

Monga nyimbo ya mtsogoleri wakale wa dziko lino malemu Bingu wa Mutharika inkanenera, mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera apempha mayiko osaukitsitsa pa dziko la pansi kuti ayende limodzi ndi mtima umodzi.

A Chakwera ayankhula izi pachiweru pomwe anatenga nawo gawo pa zokambirana za atsogoleri a mayiko osaukitsitsa pa dziko lonse la pansi omwe ukuchitikira mumzinda wa Doha mdziko la Qatar.

Iwo anati akuzindikira kuti dziko lili lonse silimasangalatsidwa kukhala losauka ndipo anaonjezera kuti ngati mayiko osaukawo akufunitsitsadi kuti akhale mayiko otukuka, onse akuyenera kugwirana manja ndikumayendera limodzi.

Apa mtsogoleri wa dzikoyu anati kugwirana manjaku kuzithandizira kuti mayikowa azitha kugawana mosavuta nzeru pa nkhani za chitukuko komaso apempha mayiko ochita bwino kuti azithandiza mayiko osaukawa.

“Ndikupempha maiko otukuka kuti athandize mayiko osauka komaso mayiko omwe amaliza maphunziro awo, ndi cholinga choti Doha Plan of Action isakhale yongolankhula chabe,” atelo Chakwera.

A Chakwera anathokozaso boma la Qatar chifukwa chochititsa msonkhanowo ponena kuti mzinda wa Qatar ndi umboni wa masomphenya omwe anachitika komaso zomwe dziko la Qatar lachita mkati mwa zaka 25, ndipo ati izi ndi zolimbikitsa kwambiri mayiko osauka.

M’mawu ake, mlembi wamkulu wa United Nations, Antonio Guterres adati chitukuko cha zachuma sichingatheke pamene mayiko ali ndi njala yachuma, akumira m’ngongole, komanso akulimbana ndi chilungamo chambiri cha kuyankha kofanana kwa mlili wa COVID-19.

Guterres anatiso chitukuko chaumunthu sichingatheke pamene maphunziro, chithandizo chamankhwala ndi machitidwe otetezera anthu akuvutika kapena kulibe komaso pamene akazi sakupatsidwa mwayi okhala mmaudindo osiyanasiyana ku ndale angakhaleso ku ntchito zina.

Iwo anaonjezera kuti ndi chifukwa chake bungwe la United Nations likugwira ntchito ndi mayiko osauka kuti likhazikitse njira zosinthira zinthu ponena kuti silingalole kuti mayiko abwerere m’mbuyo pamakwerero achitukuko atagwira ntchito mwakhama kuti akwerepo.

“Ndichifukwa chake Doha Programme of Action imaphatikizapo yunivesite yapaintaneti yopatsa mayiko anu mwayi wopeza sayansi, ukatswiri ndi ukadaulo kuti atukule chuma chambiri komanso chosiyanasiyana komanso ogwira ntchito.

“Panthawi ino yomwe anthu ambiri akusoŵa chakudya, kukhazikitsidwa kwa njira yosungiramo chakudya m’maiko osatukuka, ndi chinthu china chomwe msonkhanowu ukufuna kupanga ngati njira imodzi yothanilana ndi njala komanso kukwera mtengo kwa zakudya,” atelo Guterres.

Doha Programme of Action ikuphatikizanso kukhazikitsidwa kwa malo othandizira azachuma padziko lonse lapansi kuti athandize mayiko osatukuka komanso mayiko omwe amaliza maphunziro awo kupeza ndalama zakunja.

Follow us on Twitter:

Advertisement

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.