Tony Ngalande akhazikitsa ntchito yogulitsa chimanga m’misika yoyendayenda

Advertisement

Phungu wa nyumba yamalamulo wa dera la kumpoto m’boma la Balaka, Tony Ngalande, wakhazikitsa ndondomeko yogulitsa chimanga cha bungwe la boma logulitsa mbewu la Admarc kudzera mu misika yoyendayenda.

A Ngalande adauza nyumba yofalitsa nkhani ya Malawi24 loweluka m’mawa kuti aganiza zokhazikitsa ntchitoyi ndi cholinga chochepetsa mtunda umene anthu amayenda kupita ku msika waukulu wa Admarc omwe uli pa mchombo pa bomali komanso kuchepetsa chipwilikiti pa msikawu.

Izi zadza pamene kutsegulidwanso kwa misika ya bungwe la Admarc kwapeleka chiyembekezo chabwino pakati pa a Malawi ambiri.

Ngakhale izi zili chonchi, Malawi24 yapeza kuti masiku anayi apitawa, pa msika wa Balaka panali chikhamu cha anthu oyembekezera kugula chakudyachi zomwe zinapangitsa kuti pakhale chipwilikiti.

”Nditamva kuti izi zili chonchi, ndidaganiza zokambilana ndi akuluakulu aku unduna wa malimidwe kuti mwina tiyesele kugulitsa chimangachi kudzera mu misika yoyendayenda ndipo mwamwayi, pempho langa adalivomereza ndipo pano tayambapo ntchitoyi,” adatero a Ngalande.

Phunguyi adawonjezerapo kunena kuti pakali pano ntchitoyi ikuyenda bwino.

Pothirira ndemanga pa ndondomekoyi, Mfumu Matola ya m’bomali idayamikira phunguyi ponena kuti yachepetsa mtunda omwe anthu amayenda pokasaka chakudyachi komanso yathandizira kuchutsa anthu ambiri mu nsinga ya galu wakuda.

Ina mwa misika yomwe ntchitoyi ikugwirika ndi monga msika wa Khwisa komanso pali chiyembekezo choti ntchitoyi ichitika mu misika ya Matola,dera la mponda ndi madera ena ambiri.

Bungwe la Admarc likugulitsa chimanga pa mtengo wa K300 pa kilogalamu.

Polankhula ndi Malawi24 lachinayi, mneneri wa bugweli a Agness Chikoko adamema anthu kuti azikanena ku Polisi akawona zachinyengo zilizonse zikuchitika m’misika yawo.

Follow us on Twitter:

Advertisement

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.