Kombola kapena bomba? Nyimbo ya Namadingo yautsa mapili pachigwa

Advertisement

Chinkulirano chabuka m’masamba a mchezo pomwe anthu ochuluka akutsutsana za nyimbo yatsopano ya namandwa pamaimbidwe Patience Namadingo ya ‘Affidavit’.

Podziwa kuti lonjezo lidadulitsa mutu wa Yohane, Namadingo monga wakhala akulonjezera mmbuyo mosemu lachisanu pa 3 Malitchi, watulutsa nyimbo yatsopano yomwe akuyitchula kuti Affidavit yomweso ndiyoyamba kutulutsa mchaka chino cha 2023.

Kanema wa nyimboyi yemwe wathyakulidwa ndi mphangala yotchedwa Ronald Chikumbutso Zeleza, yemwe amadziwika bwino ndi dzina loti Ron CZ, ikuonetsa Namadingo akutsitsa mbalume zosalekeza ngati mvula yodzalira kwa chiphadzuwa china.

Wa mawu anthetemyayu yemwe wawinapo mipikisano yosiyanasiyana yochuluka, akuyiuza dona yakeyo kuti mfundo zomwe akumuuzazo wazilemba ndipo zili mubukhu laumboni ngati chisonyezo kuti adzakwanilitsa zomwe akukamba ndi kulonjezazo.

Pomwe pamatha maola anayi chitulutsileni kanema wa Affidavit yemwe zithuzi zake zajambulidwa mwapamwamba, anthu opitilira 26 sauzande anali atamuonera kale pa yuchubu (YouTube) zomwe sizimachitika chitika.

Komatu nyimboyi yadzetsa mpungwepungwe makamaka mmasamba a mchezo ochuluka pomwe anthu akutsutsana mwantu wa galu ngati nyimbo ya Affidavit ili yogwira mtima kapena ndi chulu cha ndiwo.

Anthu ena omwe athilira mang’ombe mmasamba a mchezo osiyanasiyana, ayamikira kuti nyimboyi yathyakulidwa mwa pamwamba zedi ndipo ena anafika pomuuza Namadingo kuti nyimboyi ndiyozuna moti itha kuveledwa chaka chonse.

“Doc Anavaya! Nyimbo iyiyi mwaimba zoti olo mutati musadzaimbenso ina, tidzimvera yomweyi basi,” anatelo katswiri pa zisudzo yemwe amadziwika ndi dzana loti Mr Jokes.

Naye oyimba Henry Czar wavulira chisoti Namadingo kaamba kanyimboyi ndipo anati; “Eeeh mwawina chabwino,” pomwe munthu winaso wati; “Iwe tinatopa ndikukuyamikira pano timangokuyang’ana iwe ndi katundu wa boma,”

Koma podziwa kuti makonda makonda buluzi anakonda khonde, anthu ena akuti nyimboyi ndi panja penipeni ponena kuti ilibe chikoka cheni cheni kupatula kuti kanema yake yajambulidwa mwaukadaulo kwambiri.

Gulu lina la anthu lati oyimbayu samayenera kukamiza kuika mawu ofanana mmavekedwe ponena kuti nyimbo za ‘Mapulani’ komaso ‘Pefekiti’ zinali bwino kwambiri ngakhale zinalibe mawu ofanana mmavekedwe ndipo ena ati nyimboyi siyikuveka mwachilendo kwenikweni.

“As real Namafan (ngati omutsatira weniweni), nyimboyi siili Mushe …. style mukungobwereza, this sounds like that Yewo Snippet u dropped (iyi ikuveka ngati ka nusu ka nyimbo ya Yewo), may you go back (mubwerereso) kuma styles aja U did in (munachita mu) Mapulani, Pefekiti, As tuas Pera, sakaka etc, koma izizi aah, the beat itself aah whack (ngakhale biti yakeyo aaah mbwelera), next time don’t force “rhyming”, (ulendo wina osazakakaza missed mawu ofanana mmavekedwe) keep it real! We love you Doc (timakukondani adokotala),” watelo munthu wina.

Winaso yemwe anayikira ndemanga anati: “Mwina ndimadana ndi zinthu zabwino ndineyo,” pomwe wina anaselewura ponena kuti; “mwina ndiyivereso mawa, koma kunena zoona palibe ndikuvapo ine, nde mwina nkutheka ndatopa.”

Posachedwapa Namadingo anautsa mapokoso m’masamba a mchezo pomwe anauza mmodzi mwa mkhalakale pa mayimbidwe, Lawrence Khwisa yemwe amadziwika bwino kuti Lulu mmaso muli gwa kuti iye anafika mlingo omwe Lulu sanafike pa maimbidwe.

Follow us on Twitter:

Advertisement

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.