Madzi achita katondo ku MCP: Munthali wazitaya

Advertisement

…ati ndiokhumudwa ndi kukula kwa katangale kwa boma la a Chakwera

…MCP yati a Munthali atulutse umboni pa za katangale akunenazo

Mtsogoleri wadziko lino, a Lazarus Chakwera, yemweso ndi mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress (MCP) wanyamuka lero kupita ku Qatar koma wasiya madzi atachita katondo ku chipani cha MCP.

Lachitatu anthu anadzidzimuka ndi chikalata chomwe a Munthali anatulutsa chomwe chatumizidwa kwa mtsogoleri wa dziko lino a Chakwera kuwadziwitsa za kutula pansi maudindo awo ngati mneneli wa chipani cha MCP komanso mlangizi wa mtsogoleri wa dziko lino pankhani za mtendere ndi umodzi.

Mumchikalatachi chomwe tsamba lino lawona, a Munthali ati apanga chiganizo chotula pansi ma udindo awo kaamba ka kuchuluka kwa nkhani za katangale zomwe akuti zafika pa mwana wakana phala mdziko muno.

Iwo ati ngati munthu amene ali ndi maitanidwe aubusa awona kuti nkosayenera kuti apitilire ndi ma udindo omwe anasankhidwa ponena kuti sakuona tsogolo lati boma la Tonse lingakwanitse kubweretsa chiyembekezo kwa a Malawi.

“Motsogoza pemphero ndawunikiraso ntchito yomwe ndimagwira m’boma ili lomwe lakutidwa kwambiri ndi nkhani za katangale komaso nkhani zosiyanasiyana zochititsa manyazi. Umunthu wanga wavutika kotelo kuti sindingakwanitse kupitiliza ma udindo omwe ndinasankhidwa.

“Ngakhale pali zinthu zina zomwe tachita bwino, koma ndikuona kuti ngati boma sitinapeleke utsogoleri wa bwino omwe ungakwanitse kupeleka chiyembekezo cha moyo wabwino kwa a Malawi mtsogolo muno.

“Paine ndekha ndaona kuti zomwe zikuchitikazi sizikugwirizana ndi maitanidwe anga ngati munthu okhulupilira komaso chiyembekezo chomwe anthu anali nacho pomwe ndimavomeleza ma udindo omwe ndinapatsidwa,” yatelo mbali ina ya chikalata cha a Munthali.

Iwo apempha Mulungu kuti apeleke chisomo pa a Chakwera ndi boma lonse la Tonse kuti likwanitse kuthana ndi katangale komaso mavuto osiyanasiyana amene akuti dziko lino likukumana nawo.

Koma pakuyankhapo pakutula pansi udindo kwa a Munthali, chipani cha MCP chati chilibe vuto ndi ganizoli koma chapempha mneneli wakaleyu kuti abweletse poyera umboni pa nkhani za katangale zomwe atchula mu chikalata chawo chotula pansi udindo.

Malingana ndi chikalata chomwe MCP yatulutsa chomwe wakitira ndi ogwilizira udindo wa mneneli wa chipanichi a Ezekiel Ching’oma, ngati a Munthali angapeleke umboni, zikhoza kuthandiza kuti nthambi zoyenera zichitepo kanthu pankhani yokhudza katangale akunenedwayu.

A Ching’oma atiso chipani cha MCP ndichoyamika pa ntchito yomwe a Munthali agwira pa ma udindo awo ngati ofalitsa nkhani ku chipanichi komaso ngati mlangizi wa mtsogoleri wa dziko pa nkhani za mtendere ndi umodzi.

Advertisement