A Chakwera akupita ku Qatar

Advertisement

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera, lachinayi pa 2 Malitchi akhala akunyamuka m’dziko muno kupita mdziko la Qatar komwe akuyembekezeka kukakhalako masabata awiri.

Watsimikiza za nkhaniyi ndi mkulu owona zofalitsa nkhani ku nyumba ya chifumu a Sean Kampondeni omwe amayankhula lachitatu pa nsonkhano wa atolankhani omwe unachitikira kunyumba ya chifumu ya Kamuzu mumzinda wa Lilongwe.

A Kampomdeni anauza atolankhani pa nsonkhanowu kuti a Chakwera akukakhala nawo pa nsonkhano wa mayiko osauka pa dziko lonse omwe ukachitikile mumzinda waukulu wa dziko la Qatar, Doha.

Iwo ati mtsogoleri wadziko linoyu anyamuka lachinayi m’mawa kudzera pa bwalo landege la Kamuzu mumzinda wa Lilongwe ndipo akuyembekezeka kubwelera kuno ku mudzi pa 14 mwezi omwe uno.

Mwa zina, a Kampondeni ati a Chakwera kumeneko akuyeneraso kukatula pansi udindo wawo wa wapampando wa maiko osauka pa dziko lonse omwe dziko lino linavekedwa mchaka cha 2018.

Kupatula apo, akunyumba ya boma kudzera mu chikalata chomwe atulutsa chokhudza ulendowu, ati mtsogoleri wa dziko linoyu akakhalaso akukumana ndi atsogoleri amayiko ena, atsogoleri a wabungwe komaso a bwezi pa chitukuko omwe akakhale akukambilana nawo nkhani zokhudza kutukula dziko lino.

Follow us on Twitter:

Advertisement