Dan Lu watokosola aMalawi ndi nyimbo yotukwana

Advertisement

Anthu mdziko muno makamaka mmasamba a nchezo akulavulira zakukhosi chiyamba kale pamaimbidwe, Dan Lufani kaamba ka nyimbo yake yatsopano yomwe oyimbayu wagwiritsa ntchito mawu olaura.

Munyimboyi yomwe anthu akugawana mmasamba a nchezo yomwe mutu wake ndi ‘Take My Body’, oyimbayu amene amadziwika kwambiri ndi dzina loti Dan Lu, akumuuza wachikondi wake kuti ali ndi chilakolako chofuna kuchita naye kusaweruzika.

Mmalo moonetsa unamandwa wake pa maimbidwe pogwiritsa ntchito mau ozembaitsa kapena zining’a, Dan Lu wasonyeza kuti ali ndi mkamwa mowola kwambiri kaamba koti wangoyankhula payerepayere fisi anadya mkazi wake.

Oyimbayu yemwe anaimbaso nyimbo yotchuka ya ‘Part of Life’, watchula mosapsatira mawu omwe tanthauzo lake ndi chilakolako chofuna kugonana ndi munthu, komaso zina zomwe zakwiyitsa anthu ochuluka omwe amvera nyimboyi yomwe yajambulidwa ndi Tappsy.

“Ndili ndi nye** I wanna touch it, I wanna kiss it

Ndakugubira chaka chatha, lero to night kwavuta

Baby wallah ndikumaka, I wanna see inside,

Oh my baby ndiku rocka, siine mfana ofooka

Zandigwiragwira zibaba, ndikumwera Hennessey

Koma we go go nasty, i can see you online, baby you are all mine

Ndikumwera gondolosi, zandigwiragwira zibaba

Lololo lololo, baby take my body x3

Ndili ndi nye**” Ikutelo gawo loyamba la nyimbo ya Dan Lu.

 Anthu ochuluka omwe awonera komaso kuvera nyimboyi, adzidzimuka ndi chichewa chomwe oyimbayu wagwiritsa ntchito ndipo ambiri ati izi mzochititsa mayazi potengera kuti nyimbo yoyimililitsa mapilikaniroyi watulutsa ndi nzira zembe yemwe amayenera kukhala chitsazo chabwino kwa achisodzera omwe ayamba kumene kuyimba.

“Aaaaaaa koma zoona??? Komatu ali ndi mwana Dan yu tsono azimvera zimenezo? Imagine anzake ku school aziti iwe bambo ako ati ali ndi nye..,” watelo munthu wina patsamba la fesibuku.

Munthu winaso wati: “Oyimba akuluakulu ngati mwatopa ndi kuyimba ndi bwino mungonena. Nanga mpaka ndili ndi nye.. I wanna touch it. Ayi fenks.”

Nyimboyi siyinamudutse Joshua Chisa Mbere amene amayankhula pa zinthu zosiyanasiyana pa mmasamba ake anchezo yemwe wati: “Dan Lu watilaula. His song; Take My Body ndi Malaulo. I can’t play that song in my house. I’m by birth a strict moralist. (Sindingasewere nyimboyi mnyumba mwanga. Ndinabadwa ndi ulemu). Dan Lu, Thank for the Song. But No Thank You.”

Pakadali pano anthu akuthamangira kutsamba la fesibuku laoyimbayu komwe akumutafunira lilime kaamba ka nyimboyi ndipo munthu wina kumeneko wati;

“Daniyele eti mwaimba inayake yopoila dzulo, fans ati mumvela nokha m’nyumba mwakwanu komweko.”

Koma ngakhale zili chonchi, anthu ena akumuikira kumbuyo Dan Lu ati ponena kuti nyimboyi siyotukwana kwenikweni kuyelekeza ndi nyimbo zina zakunja zomwe a Malawi akhala akuvera.

“Chigulu chakwiya ndi nyimbo ya Dan Lu. Koma mongokumbutsana tinkamvera achina Sexual Healing, Candy Shop, Lollipop,” watelo munthu wina pothilira ndemanga za nkhaniyi.`

Follow us on Twitter:

Advertisement