Tibaye nawo galu – wamangidwa ku Lilongwe kamba kogulitsa kanyenya wa galu

Advertisement

Ngati muli bwenzi wa ziwaya za nyama mu Lilongwe, ndi kutheka munadya kale galu wanu. Maka anthu amene mumakonda kubaya ya mbuzi.

A polisi mu mzinda wa Lilongwe amanga bambo Andrew Mthiko a zaka 38 kamba kowaganizira kuti akhala akudyetsa ma kasitomala awo nyama ya galu kumati ndi ya mbuzi.

Malinga ndi maripoti ochoka ku Polisi, bambo Mthiko amangidwa pachiweru atapezeka akukonza galu cholinga akagulitse ku msika kwa makasitomala awo okonda mbuzi.

A Mthiko ati amachita malonda awo ku madera a 24 ndi ena ozungulira komwe amanka nayenda ngati bambo ogulitsa mbuzi.

Padakali pano a bambo Mthiko ali m’manja mwa a polisi ndipo ati awatengera kubwalo kuti akayankhe mlandu odyetsa anthu zinthu zosayenera.

Maiko ena nyama ya galu imadyedwa ndithu koma ku Malawi anthu ambiri amachita nayo khambi.

ollow us on Twitter:

Advertisement