Sindingasiye anthu anga akufa ndi Kolera ine kumakadyelera ku Ethiopia – Chakwera atuma nduna ku msonkhano wa AU

Advertisement

Ngati mumayesa mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ndi osalabadira a Malawi, mukuyenela kusintha maganizo. Ngati mumaona ngati mavuto akhuthukira pa dziko lino a Chakwera sakuwaona ndiye mwina mumangowalakwira.

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera watuma nduna yake yoona za ma ubale a dziko lino ndi maiko ena a Nancy Tembo kuti akamuyimilire ku dziko la Ethiopia pa msonkhano waukulu wa mayiko a mu Africa, AU.

Izi zachitika pamene dziko la Malawi likudutsa mu mavuto osiyanasiyana kuphatikiza kusefukira kwa madzi, matenda a Kolera, kuthima kwa magetsi ndi kukwera mitengo kwa zinthu.

Malinga ndi chikalata chimene a ku nyumba ya boma atulutsa, a Chakwera akhala otanganidwa masiku ali nkudzawa kuti apezeke apita ku msonkhanowu ku Addis Ababa.

“Mwa zina, a Chakwera akhala akukumana ndi nduna kunka akulondondoloza ndondomeko ya budget imene boma lawo lipereke ku nyumba ya malamulo masiku akubwerawa,” atero a boma.

A Chakwera akhala akudzudzulidwa kamba kokhala ndi dyera pa ma ulendo ngakhale pa nthawi imene mavuto achuluka mu dziko. Tsopano zikukhala ngati iwo amvera madando a anthu a mu dziko lino.

Advertisement