Chaka chino umwedwa: Castel yabweretsa mabotolo otsika mtengo

Advertisement

Anthu omwa zakumwa zaukali omwe amalephera kukonkha kukhosi kaamba kochepekedwa mthumba, ali ndi chimwemwe tsaya kaamba koti kampani ya Castel Malawi yalengeza kuti yabweretsa mabotolo atsopano azakumwa zawo zina omwe ndi a mitengo yofikilika.

Kwa nthawi yaitali mbiyang’ambe zochepekedwa mthumba mdziko muno, zakhala zikulephera kumwa wina mwa mowa omwe kampani ya Castel imapanga kaamba koti mitengo yake inali yokwelerako, ndipo ambiri akhala akumwa mowa odula pochita kugulilidwa ndi anthu achifundo.

Mwachitsanzo, mtengo ovomelezeka wa botolo la 750m la Malawi Gin komaso Malawi Vodka ndi K9,000, pamene mowa wa Premier Brandy mtengo ovomelezeka unali K12,000 koma mmalo ena zakumwazi zimagulitsidwa mitengo yokwera kuposa apa, zomwe zakhala zikupangitsa anthu ambiri kulephera kufikira zakumwazi.

Koma zonsezi ndi mbiri ya makedzana tsopano kaamba koti kampani ya Castel yati yabweretsa mabotolo a mlingo wa 330ml a mowa wa Malawi Gin, Malawi Vodka komaso Premier Brandy omwe ndiotsikirako mtengo.

Chikalata chomwe kampani ya Castel yatulutsa chonwe wasainira ndi wachiwiri kwa mkulu owona nkhani za malonda a Nelson Zoto Banda, botolo la Malawi Gin komaso Vodka la mlingo wa 330ml, lizigulitsidwa pa mtengo wa Mk2,500 pamene botolo la 330ml la Premier Brandy lizigulitsidwa pa Mk4,500.

“Pamene tikupitilira kupanga ndikubweretsa katundu wabwino pamsika, ndife okondwa kubweretsa milingo ya tsopano ya mowa wathu. Milingo imeneyi tikungoonjezera pa milingo yomwe ilipo kale ndipo mowa wake ndi omwe mukuudziwa kalewo,” watelo Banda mu chikalata.

Kampani ya Castel kudzera kwa Banda, yati lingaliro lobweretsa milingo ya tsopano yadza pofuna kufikira anthu ochuluka omwe akhala akulephera kugula mowa wawo kaamba kochepekedwa ndalama.

Malingana ndi a Banda, anthu amene azigulitsa mowa wa mabotolo a tsopanowa, azipanga mphindu lokwana K11 pa K100 iliyose ndipo ati izi sizikutanthauza kuti mowa wa milingo ya 750ml ayichotsa pansika koma atsindika kuti milingo yonseyi izigulitsidwa limodzi.

Pali chiyembekezo kuti kampani ya Castel ikhazikitsa milingo ya tsopano ya mowayi pa 26 mwezi uno pa mwambo omwe ukachitikire pa Grand Business Park mu mzinda wa Lilongwe komwe kukakhaleso zosangalatsa zosiyanasiyana.

Pakadali pano, anthu mdziko muno makamaka mmasamba a mchezo akupeleka maganizo osiyanasiyana pakubweretsedwa kwa milingo yochepelayi ndipo pomwe ena akuti izi mzabwino, ena akuti izi zipangitsa kuti ena amene samamwa mowa ayambe ku mwa kaamba kwa mitengo yosaboola mthumbayi.

Ena ati uwu ndi mwayi oti mbiyang’ambe zochepekedwa zomwe sizinamweko mowa odula monga wa Premier Brandy, ziulaweko ponena kuti Mk4,500 ndi ndalama yofikilika kuyelekeza ndi Mk10,000 ya botolo lalikulu.

Follow us on Twitter:

Advertisement