Mnyamata wapezeka atamwalira mu nyumba ya chibwenzi ku Phalombe

Advertisement
Malawi24.com

Mnyamata wa mu folomu yachiwiri pa sukulu ina ya sekondale ku Phalombe wapezeka atafa ku nyumba ya chibwenzi chake komwe anakagona.

Apolisi a ku Phalombe atsimikiza za nkhaniyi ndipo ati mnyamatayu dzina lake ndi Joseph Madeya yemwe amachokera m’mudzi wa Ntchedzinga, mfumu yaikulu Mkanda ku Mulanje.

Malingana ndi oyankhulira apolisi ku Phalombe, a Jimmy Kapanja, mnyamatayu anakagona ku nyumba ya mkazi wake.

M’mawa mwake, mkaziyu sanapite ku nchito ndipo abwana ake anamulondola ku nyumba kuti akamve chifukwa chomwe sanapitile ku nchito.

Abwanawo anakapeza mtsikanayo akuoneka odwala ndipo mnyamata yemwe anali naye atakomoka.

Mnyamatayo anamutengela kuchipatala komwe adokotala ananena kuti wamwalira ndi poyizoni.

Pakali pano, thupi la mnyamatayo alitengela ku chipatala chachikulu cha Queen Elizabeth ku Blantyre kuti akaliyeze.

Mtsikanayo akulandira thandizo ku chipatala cha Phalombe.

Follow us on Twitter:

Advertisement

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.