Mikango yachuluka, ikufunika njira zakulera – yatelo African Parks

Advertisement

Bungwe la akatswiri owona za kasamalilidwe ka nyama zakutchire la African Parks lati likufuna lipemphe boma la Malawi kuti liyambe kugwiritsa ntchito ndondomeko ‘yakulera’ pa mikango ponena kuti yayamba kuchulukana kwambiri maka mu nkhalango yotetezedwa ya Majete.

Izi ndi malinga ndi nyuzipepala ya pa intaneti ya The Investigator.news yomwe nkati mwa mwezi uno inatulutsa nkhaniyi potsatira kuyankhulana kwawo ndi akuluakulu a African Parks lomwe ndi bungwe lomwe likuthandiza boma kusamalira nkhalango zotetezedwa za Majete, Liwonde ndi Nkhotakota.

Malingana ndi nyuzipepalayi, mkulu wa African Parks kuno ku Malawi a Samuel Kamoto, ati pakadali pano ku nkhalango yotetezedwa ya Majete kuli mikango makumi asanu (50) chomwe akuti ndichiwerengero chochuluka kwambiri.

A Kamoto anati ngati njira imodzi yosamalira nyamazi komaso nyama zina mnkhalangoyi, nkofunika kuti boma lipeleke chilolezo kuti akatswiri apeleke mankhwala akulera ndi cholinga choti nyama zoopsazi zisapitilire kuchulukana kwambiri.

Iwo anatiso ngati boma silingalore kuti mikangoyi ipatsidwe mankhwala akulerawa, ndi kwabwino kuti bomalo lisamutsire ina mwa mikangoyi ku nkhalango zina zomwe zili zotetezedwa bwino koma anena kuti njirayi ndiyopeleka chiopsezo kaamba koti nkhalango zambiri mdziko muno zilibe mipanda yoyenelera.

Poyankhapo pa pempholi, mkulu wa nthambi yowona za nkhalango ndi nyama zakutchire a Brighton Kumchedwa, ati pakadali pano boma silinaganizepo zogwiritsa ntchito njira ina iliyonse yochepetsera chiwerengero cha mikangoyi kupatula kuyisamutsira ina mwa iyo ku nkhalango zina.

Iwo anati African Parks isade nkhawa ndi kusoweka kwa mipanda ku nkhalango zina kamba koti pali njira zambiri zomwe zingatsatidwe.

A Kumchedwa anatinso m’buyomu African Parks adapemphapo kuti ayambe njira za kulera pa Njobvu zomwe zachulukananso kwambiri koma adawakaniza pozindikira kuti pali nkhalango zambiri zomwe zikufunika zitabwereranso mchimake ndipo potsatira kukanizaku, Njobvu 263 anazisamutsira ku malo osungirako nyama a Kasungu National Park.

Nkhaniyi inatuluka pomwe bungwe la African Parks linakonza msonkhano omwe cholinga chake kunali kufuna kudziwitsa anthu omwe amagwira nawo ntchito limodzi momwe ntchito zawo zayendera mchaka chathachi.

Follow us on Twitter:

Advertisement