Chakwera akufuna kuchotsa Chizuma kudzera mwa anthu ena – Kalindo

Advertisement

…wayitanitsa zionetsero ku Mulanje

A Bon Kalindo ati zomwe zikuchitika pankhani yakumangidwa kwa mkulu wa ACB a Martha Chizuma, ndi chinyenga aphunzitsi ndipo ati zili ngati mfiti yomwe imamupha munthu ndipo yomweyo imakaliraso kwambiri pa maliro a munthu yamuphayo kuti isadziwike kuti yapha ndiiyo.

A Kalindo amayankhula izi potsatira zomwe anayankhula mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera omwe lachitatu sabata ino anaphera mphongo zomwe lapeza gulu lomwe limafufuza za kumangidwa kwa a Chizuma kuti palibe akuluakulu aboma omwe akudziwapo kanthu za kumangidwa kwa a Chizuma chaka chatha.

Muuthenga wawo omwe anthu akugawana m’masamba a mchezo, a Kalindo ati zomwe zinayankhulidwazi ndi bodza lamkunkhuniza ndipo ati zikuchitikazi ndi chinyenga aphunzitsi ponena kuti apolisi omwe anakamanga a Chizuma sangapange zimenezo mwaokha ndipo atsindika kuti a Chakwera nawoso akudziwapo kanthu zankhaniyi.

Apa a Kalindo ati mtsogoleri wadziko linoyu akungofuna kudzionetsa ku mtundu wa a Malawi ngati kuti sakudziwa kanthu ndipo anati izi ndi chimodzimodzi zomwe mfiti yoti yapha munthu imapanga ikafuna kuti anthu asazindikire kuti chipongwecho yapanga ndiiyo.

“Mfiti ikamufuna munthu imapeza njira yomuphera. Zimene wakamba Chakwera pa 18th January, 2023 ndichimozimodzi mfiti kulira pa maliro koma itapha iri iyo. Chenjerani Amalawi chikupangika pa nkhani ya Martha Chizuma ndi chinyenga mphuzitsi.

“Chomwe chikuchitika apa ndikufuna kutipusitsa a Malawi. Chakwera akufuna amuchotse Martha pa udindo wake kudzera mwa anthu ena. Akufuna azichosemo pa nkhani ya Martha kuti pa mawa zizaoneke ngati anamuchotsa pa udindo ndi anthu odana naye, ngati kuti mwini filimu si iyeyo,” anatero a Kalindo.

Iwo anaonjezera kuti kuchotsedwa kwa a Steve Kayuni paudindo wawo ndikokaikitsa ponena kuti ali ndi chikhulupiliro posachedwapa pompa kuti a Kayuni atha kupatsidwa udindo wina m’boma ngati chipukuta misozi pa zomwe zachitikazi.

Pakadali pano a Kalindo alengeza kuti achititsa zionetsero zokwiya ndi boma la Tonse lachisanu sabata yamawa kutsatira kutha kwa masiku khumi omwe anapeleka kwa mtsogoleri wadziko lino a Lazarus Chakwera ndi lachiwiri wawo a Saulos Chilima kuti akhale atatula pansi udindo.

Izi zikudza pomwe a Kalindo pamodzi ndi mzika zina zokhudzidwa anapeleka masikuwa kuti atsogoleri awiriwa atule pansi udindo ponena kuti alephera kuyendetsa dziko lino komaso kuthetsa mavuto omwe anthu akukumana nawo tsiku ndi tsiku.

Iwo anawopseza kuti ngati a Chakwera ndi a Chilima satula pansi udindo wawo, pofika lero lachisanu, iwo amemeza anthu mdziko muno kuti awonetse mkwiyo wawo kudzera ku zionetsero zomwe akuzitchula kuti Payerepayere.

Potsatira kusatula pansi kwa a Chakwera ndi a Chilima, a Kalindo alengeza kuti akuyamba kuchititsa zionetsero ndipo ati ziyambira m’boma la Mulanje lachisanu sabata yamawa, pa 27 January zomwe akuti cholinga chake ndikukakamizabe atsogoleri awiriwa kutula pansi ma udindo awo.

“Zionetsero zilipo ku Mulanje lachisanu pa 27 January ndipo tikayambira pa Chisitu mpaka kukafika pa boma kwa a DC. A Malawi tinaombera mfiti m’manja osadziwa. Zimene zikuchitika mdziko muno ndizovetsa chisoni kwambiri. Mtsogoleri amayenera mukhala munthu oti azikhulupililidwa ndi anthu,” anatero a Kalindo.

Pakali pano, mzika zokhudzidwazi zalembera kalata akuluakulu akhonsolo ya boma la Mulanje kuwadziwitsa za dongosolo la laziwonetsezi ndipo pali chiyembekezo kuti akamaliza kumeneko, zionetserozi zichitikaso m’bomala Chikwawa masiku akubwelawa.

Follow us on Twitter:

Advertisement