Apolisi awapempha kuti athane ndi omwe amatulutsa makalata abodza

Advertisement

Woyankhulapo pankhani zochitika m’dziko, a George Chaima, apempha a polisi kuti athane ndi aliyense opezeka akulemba makalata a bodza okhudza andale komanso anthu ena.

Iwo alankhula izi pomwe a polisi akhazikitsa kafukufuku ofuna kupeza anthu omwe anatulutsa kalata yabodza yofotokoza zakutula pansi udindo kwa mtsogoleri wachiwiri wa dziko lino a Saulos Klaus Chilima.

A Chaima apempha anthu omwe amachita izi kuti asiye chifukwa zimabweretsa mavuto pa chuma, kakhalidwe ka anthu komanso zili ndikuthekera kobweretsa kusagwirizana pa ndale mdziko muno.

Masiku apitawa mdziko muno mwakhala mukutuluka  makalata, omwe ena mwa iwo amafotokoza zakutula pansi udindo kwa wachiriwi kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima, kudwala kwa mtsogoleri wa kale wa dziko lino a Arthur Peter Mutharika komanso ina imafotokoza zokhudza chipani cha Malawi Congress Party kuti chatulutsa chikalata cha maina omwe mtsogoleri wa dziko lino akuyenera kuwasankha ngati nduna za tsopano.

Follow us on Twitter:

Advertisement

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.