Zamkutu! Gwengwe wati a Malawi ayiwale za K7 thililiyoni ya Bridgin

Advertisement

Pomwe anthu anali ndichiyembekezo kuti zinthu zambiri zitha kuyamba kuyenda bwino kaamba ka ndalama yokwana K7 thililiyoni yomwe bungwe lakunja la Bridgin Foundation limayenera kupeleka ku dziko lino, nduna ya zachuma a Sosten Gwengwe athira mchenga mu mmemo wagulo ponena kuti mgwirizanowu unali zamkutu zenizeni.

Pa 28 November chaka chatha a Gwengwe anasainira mgwirizano ndi bungwe la Bridgin Foundation lomwe akuti limayenera kupeleka ku dziko lino ndalama zokwana 6.8 biliyoni zaku America zomwe ndikupitilira K7 thililiyoni zomwe a kuti zimayenera kugwira ntchito yotukula dziko lino.

Mwa zina, gawo lina la ndalamazi akuti limayenera kugwira ntchito yomanga sukulu yaukachenjede ku Mzuzu komaso sukulu yapamwamba yophunzitsira madotolo ndi zina zambiri zomwe a kuti zikanapangitsa dziko lino kufika pamlingo wina pankhani za chitukuko.

A Malawi ochuluka kuphatikizapo akatswiri a zachuma anayamikira boma la mgwirizano wa Tonse motsogozedwa ndi a Chakwera kaamba kandalamazi zomwe nduna ya zofalitsa nkhani a Gospel Kazako anauza dziko lino kuti zabwera kaamba ka maulendo a kunja omwe a Chakwera anayenda kumapeto kwa chaka chatha.

Komatu paja ukatambatamba uziyang’ana kummawa kungakuchere! Zadziwika tsopano kuti zonsezi anali maloto achumba kaamba koti a Gwengwe omwe adasainira mgwirizanowu kunyumba yachifumu ya Kamuzu ku Lilongwe, abwera poyera ndikuliuza dziko kuti palibe amene anasainira mgwirizanowu.

Ndunayi imayankhula izi mu mzinda wa Lilongwe pomwe imatseka zokambirana zamkumano wa magulu osiyanasiyana omwe amapeleka maganizo awo pa ndondomeko ya zachuma ya chaka cha 2023/2024 ndipo anati Bridging Foundation inabwera kudzasewera.

“Kulibe anasainira kuti kwabwera ndalama 6.8 biliyoni za ku America ya chanimchani, zimenezo ndizamkutu chabe. Nkhani zenizeni ndi zomwe tikukambilana panozi. Osati kudzangosewera kuti Bridgin Foundation chanimchani. Zimenezo ndizamkutu zisiyeni. Fuso lenileni ndiloti kodi titha kukhala ndi ndondomeko ya zachuma yokomera mbali zonse?” Atelo a Gwengwe.

Izi zikudza ngakhale kuti anthu ochuluka analichenjeza boma la Malawi kuti lisaphethile pa mgwirizanowu ponena kuti bungwe la Bridgin Foundation litha kukhala la a tsizina mtole kaamba silimaonetsa zizindikiro zoti ndi bungwe lenileni.

Pakadali pano m’modzi mwa anthu omwe anadzudzulapo boma posainira mgwirizanowu, a Joshua Chisa Mbele, awulura kudzera patsamba lawo la mchezo la fesibuku kuti pa nthawi yomwe iwo anadzudzula boma zakusainira mgwirizanowu, anaopsezedwa kuti aphedwa.

“Mneneri anatukwanidwa zakusi. Kuopsezedwa kuphedwa pangozi ya galimoto chifukwa chofotokoza kuti Bridgin Foundation ndiya mbava. Mpaka ndidanena kuti muone Chidendene cha Nsapato ya munthu wamkulu wa Bridgin. Chinali Chopotoka. Chotopa ndi Kugaula nthaka,” atelo a Chisa Mbele.

Follow us on Twitter:

Advertisement