Chakwera? Haaa ndiye bola Mayi JB – atero a Malawi pa tsamba la Mneneri

Advertisement

Alibe moto Chakwera

Mu kufanizira atsogoleri amene Malawi wakhala nawo mu zaka zapitazi, mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera akuoneka alibiletu moto moti a Malawi sakufunanso kumva za iwo.

Pa mfunsafunsa amene wachitika pa tsamba la pa Facebook la Joshua Chisa Mbele amene omukonda amamutcha Mneneri, a Malawi ochuluka aonetsa kutsakhutitsidwa ndi a Chakwera.

“Kodi pa malikisi 10, aliyense mwa atatu awa mungawapatse angati?” anafunsa motero a Mbele kenako ndi kuyika mayina a Mayi Banda, Polofesa Mutharika ndi a Chakwera.

Anthu oyankha aonetsa kuti a Mutharika ndi otsogola pa atsogoleri atatuwa pamene a Chakwera ndi chitsekakhomo.

Pamene anthu ena akhala akupatsa Mayi Banda malikisi 5 pa 10, ena akhala akupatsa Chakwera 0 amene pa 10.

Ngakhale a Malawi ochuluka anachita zionetsero kuti a Chakwera alowe m’boma, zikuoneka kuti mkuluyi alibe chikoka.

Mavuto a za chuma, katangale komanso kusamvera malango ndizo zakwiyitsa a Malawi ochuluka ndi utsogoleri wa a Chakwera.

Advertisement