Oba ndalama za boma adwala nthenda zikuluzikulu – watero mneneri Mbewe

Advertisement

…wati boma la Tonse lidzipita, ndi la bodza

Mtsogoleri wa gulu la Freedom of Worship and Economic Liberation (FOWEL) mneneri David Mbewe walavula zakukhosi powauza atsogoleri a mgwirizano wa Tonse kuti ndalama za boma zomwe akuba adwala nazo nthenda zikuluzikulu, ndipo wati azilavula popita zipatala zakunja.

Mneneri Mbewe amayankhula izi Loweruka usiku pamene mpingo wawo wa Living Word Evangelical Church (LIWEC) unachititsa mapemphero awusiku olowera chaka chatsopano cha 2023 komwe asambitsa chokweza akuluakulu a mgwirizano wa Tonse omwe wati akuba ndalama za a Malawi zomwe zikanatha kutukula dziko lino

Mneneriyu anayamba ndikudzudzula atsogoleri a boma la Tonse omwe wati ananamiza anthu mdziko muno nthawi yokopa anthu kuphatikizapo kuwauza kuti mgwirizano wawo ukazalowa m’boma, anthu azizadya katatu komaso kuwauza kuti azagula feteleza pamtengo osapitilira K5000.

A Mbewe amene munkanema yomwe anthu akugawana mmasamba anchezo amaoneka okwiya kwambiri, ati boma la Tonse lalephera kukwanilitsa zomwe linalonjeza kwa anthu nthawi ya kampeni ndipo ati lipakile katundu wake ndipo lizipita, lisawatengele a Malawi pamgong’o.

“Boma ili ndi la bodza ndipo likuyenda tsiku ndi tsiku pogwiritsa ntchito bodza. Simungatinamize kuti tidzagula feteleza pa mtengo wosapitilira K5000 pamene pano ali pa mtengo wa pafupifupi K80,000 ndipo tikumachitaso kugonera komko, feteleza akusowa.

“Boma ili linatinamiza, ndipo boma ili ngati likulephera kulamulira anthu, apakile ndipo adzipita, adzipita. Ngakhale mu baibulo, mafumu amene amalephera kulamulura bwino mtundu, amatula pansi udindo. Asiyeni a Malawi osawazuza mwa ntundu uwuwu,” atelo a Mbewe.

Iwo anakumbutsa boma la Tonse kuti linalonjeza kuti lizathetsa mchitidwe owaimitsa apolisi pansewu kwa maola ochuluka mtsogoleri wa dziko akamadutsa komaso nkhani yosangalatsa aphunzitsi powapatsa zowayenereza kuti azilimbikira ntchito zomwe a kuti mpaka pano sizikuchitika.

Munthu wa Mulunguyu yemwe anati sakuopa kuphedwa kaamba koti anafa kale, wati panopa agwada pansi kupemphera kuti Mulungu alange onse omwe akuba ndalama za boma zomwe zikanatha kutukula dziko lino, ndipo mwantu wagalu wamenyetsa nkhwangwa pamwala kuti a Malawi sangapilire ngati momwe akuluakulu aboma ena akhala akuuzira anthu mdziko muno.

Apa a Mbewe omwe anati ndizokhumudwitsa kuti maiko omwe azungulira Malawi akupita patsogolo pomwe dziko lino lili pamodzi modzi, anenera kuti onse omwe akuba ndalama za boma, adwala nthenda zikuluzikulu ndipo “mbavazo” zizipita zipatala zakunja komwe akuti azikapeleka ndalama zomwe amabazo.

“Musadandaule, mfumu iliyonse yoipa, mumdzina la Yesu, isapeze mtendere. Mfumu iliyose ya bodza mudzina la Yesu Mkhristu Mnazarayo ndati isapeze mtendere. Ndalama zimene mwabazo muzipita nazo kuchipatala ndipo matenda ake azikhala akuluakulu okhaokha mpaka ndalama zimenezo zitha psitii,” anatelo ndine polofeti David Mbewe.

“Muli ndi BP, muli ndi shuga, mupite ku India, mupite England, mutha ma miliyoni ambirimbiri, ndalama zimenezo mulavura. Lero anthu akudwala kolera akugona mchipatala pansi popanda bedi, popanda matilesi, komaso osadya,” anaonjezera choncho a Mbewe.

A Mbewe anapitilira ndikunena kuti iwo si munthu wa ndale koma ati iwo ndi munthu amene akufuna kuti a Malawi alinjoye dziko lawo osati kukhalira m’mpanthi, ndipo ati atafuna kukhala munthu wa ndale, palibe chipani chomwe chingamake, ati atha kumaliza zipani zonse mdziko muno.

Iwo alangiza anthu mdziko muno kuti asamayambe ndale ndi cholinga chofuna kulemera ponena kuti maganizo ngati amenewo ndi amene akupangitsa kuti dziko lino lizikhala ndi azitsogoleri akuba ndalama za boma.

“Pano mungopita ku paliyamenti kumakakangana, mpaka kumapempha ndalama ya alawasi ya madalaiva, muli phee, kufuna kulemera. Mudzipemphera kuti kutsogolo kuno oyamba ndale aziyamba olemera okha okha osati akapita ku ndale azikaba ndalama,” ateloso a Mbewe.

Iwo anati sakuikila kumbuyo chipani cha DPP ndipo chipanichi nacho chanalinamiza dziko kuti lidzakhala ngati Singapore, zomwe akuti sizikusiyana ndi zomwe mgwirizano wa Tonse ukunena kuti dziko lino lili paulendo wa ku Kenani, zomwe ati nzosatheka kaamba kamomwe zinthu zikuyendera mdziko muno.

Follow us on Twitter:

Advertisement