Anthu ena omwe akudwala kolera akumakana kupita kuchipatala – adandaula a zaumoyo

Advertisement

Nduna ya zaumoyo a Khumbize Kandodo Chiponda yapempha mafumu, atsogoleri amipingo komanso achitetezo kuti azidziwitsa achipatala msanga akadziwa kuti pali ena omwe akubisa munthu yemwe ali ndi zizindikiro za kolera.

Muchikalata chomwe atulutsa dzulo, a Chiponda ati anthu ena omwe ali ndi zizindikiro za kolera monga kusanza ndikutsekula m’mimba akumakana kupita kuchipatala.

Malingana ndi a Chiponda, atsogoleri ena amipingo akumakaniza mamembala awo kupita kuchipatala kukalandira thandizo pazifukwa za zikhulupiririo za zipembedzo.

“Pachifukwa ichi mwatsoka tikumataya miyoyo ya anthu omwe anali ofunika pachitukuko cha dziko lino chonsecho imfa zotero tikadatha kuzipewa tikadathamangira nawo kuchiptala kuti akalandire thandizo loyenera msanga,” antero a Kandodo.

Iwo apempha atsogoleri monga mafumu ndi azachipembedzo kuti azitengapo gawo pothetsa mchitidwe okana kuchipatala ndi kuti azilimbikitsa anthu kutsatira njira zoyenera zopewera kolera.

Iwo apemphanso anthu mdziko muno kuti akhale ndi chizolowezi chomafufuza momwe ena alili tsiku ndi tsiku.

Kuno ku Malawi kolera inayamba kufala mu March chaka chatha ndipo yapha anthu okwana 576. Dzulo lokha, anthu okwana 464 ndi omwe anawapeza ndi kolera.

Follow us on Twitter:

Advertisement