A Malawi kuchulukana ngati mchenga: ana 1,628 abadwa tsiku la khisimisi lokha

Advertisement

Pokwanilitsa mau omwe amapezeka m’buku lopatulika pa Genesesi 1 ndime ya 28, lomwe limati; ‘Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, mucuruke, mudzaze dziko lapansi,’ zadziwika kuti ana okwana 1,628 ndi omwe abadwa mdziko muno tsiku la khisimisi lokha.

Izi ndi malingana ndichikalata chomwe unduna wa zaumoyo watulutsa sabata ino chomwe chasonyeza kuti pa 25 December lomweso ndi tsiku lomwe anthu amakumbukira kubadwa kwa Yesu Mkhristu, ana 1,628 abadwa mumzipatala za mdziko muno.

Chikalatachi chikusonyeza kuti pa chiwerengerochi, ana okwana 835 ndi akazi pamene 793 otsalawo ndi ana amuna.

Malingana ndi undunawu, boma la Lilongwe ndi lomwe lili ndi chiwerengero chochuluka ndipo zadziwika kuti ana 258 ndi omwe abadwa patsikuli kumeneko ndipo nalo boma la Blantyre akuti lalandira mphatso ya ana okwana 111.

Maboma a Zomba (109), Mangochi (96), Kasungu (92) ndi Ntcheu (79) ndi maboma ena omwe alandiranso ana ochuluka.

Boma la Rumphi lili ndi chiwerengero chocheperako kaamba koti zadziwika kuti kumeneko kwabadwa ana okwana 18 okha pamene boma la Neno kwabadwa ana 20, ndipo mwa chiwerengerochi, 12 ndi amuna pamene 8 enawoso ndi akazi. Koma chiwerengero chochepa kwambiri chili ku Likoma komwe kwabadwa mwana m’modzi ndipo ndi wamkazi.

Ngakhale kuti akulu anati kuchulukana mkwabwino koma kuipira kutha ndiwo m’mbale, chiwerengero cha ana omwe abadwa pa khisimisichi chitha kukhala choposera pamenepa kaamba koti ana ena amatha kubadwira mmanyumba osati kuchipatala, choncho amenewo sanawerengedwe nawo.

Malingana ndi kafukufuku yemwe anachitika mchaka cha 2018, dziko lino lili ndi anthu okwana 17.5 miliyoni koma pano pena a kuti chiwerengerochi chitha kufika pa 20 miliyoni tsopano.

Follow us on Twitter:

Advertisement