Boma lavomereza kuti likusowa makobiri olipilira mafumu

Advertisement

Pa galaundi pateleleratu pamene boma lavomereza kuti lilibe makobiri okwanira kuti lilipire mafumu ena mu dziko muno.

Polankhula munyumba ya malamulo lachiwiri lapitali, nduna yoyang’anira za maboma ang’onoan’gono Blessings Chinsinga adauza nyumbayi kuti vuto li ladza kamba kosowa ndalama.

Nduna yi idanena izi pame imayankha funso kuchokera kwa Phungu wa Zomba Ntonya, Ned Phoya. Phungu yu, adafunsa a Chinsinga pankhani yokhudzana ndi mavuto amene ena mwa mafumu akukumana nawo.

A Chinsinga adaonjezeranso kunena kuti boma likukonza ndondomeko yoti litukule maboma kuti azizipangira ndalama zokwanira. Komanso, mafumu ambiri akhale nawo mugulu lolandira mswahala.

Malingana ndi a Chinsinga, pakali pano boma limalipila mafumu 42,450 zomwe zimafunika ndalam zokwana K3.2 biliyoni pa chaka. Iwo anaonjezera kuti pali mafumu ena 9,000 oyenera kuti azilipidwa ndipo akudikira kuti awayike pa mndandanda wa mafumu oyenera kulandila ndalama.

A Chinsinga adapemphanso andale kuti asiye kulowelera nkhani zokhuzana ndi mafumu popeza zitha kubwelesa chisokonezo.

Advertisement