Amwene, ndapita – Mwenifumbo watuluka UTM

Advertisement

Watsatira Winiko, naye kudzisiya. Amene anali mneneri wa chipani cha UTM, a Frank Mwenifumbo, atsanzika kwa mtsogoleri wa chipanichi, a Saulos Chilima.

Malinga ndi chikalata chimene Malawi24 yaona, a Mwenifumbo ati iwo atula pansi udindo wawo ndinso atuluka chipani cha mu boma cha UTM.

“Ndaona kuti ndikapange zina, ndayamba ndapuma ku ndale,” alemba motelo a Mwenifumbo.

Iwo ati akhala akufuna kutsanzika koma amalephera kamba koti Mayi Chilima akhala asakupeza bwino. Tsopano, iwo ati basi aona kuti ndi bwino alondole msana wa njira.

A Mwenifumbo achoka pamene zikuoneka kuti ubale wa chipani cha UTM ndi MCP suli bwino konse.

Advertisement