Azungu andidalira — Chakwera

Advertisement

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera wati zomwe lapanga bungwe la IMF povomeleza kupeleka kudziko lino ndalama zokwana pafupifupi K90 billion, ndichisonyezo choti mabungwe akunja ayambiraso kukhulupilira dziko lino pansi paulamuliro wawo pakayendetsedwe ka chuma.

Izi zikudza pomwe sabata ino bungwe la International Monetary Fund (IMF) lomwe limayang’anira nkhani za zachuma padziko lonse, lalengeza kuti lapeleka ndalamazi ku boma la Malawi pansi pa ndondomeko ya Rapid Credit Facility (RCF).

Poyankhulapo pa nkhaniyi kudzera m’masamba a mchezo a fesibuku komaso twita, a Chakwera ati iyi ndi nkhani yosangalatsa kwambiri yomwe mMalawi aliyese akuyenera kusangalatsidwa nayo ponena kuti ndalamazi zithandiza zinthu zochuluka mdziko muno.

Mtsogoleri wa dziko linoyu wati, ndalamazi zithandiza kuti dziko lino lithane ndi mavuto osiyanasiyana azachuma komaso mavuto angozi zogwa mwadzidzidzi.

Iwo atiso thandizoli ndichisonyezo choti mabungwe a kunja kwadziko lino komaso abwezi a dziko lino pankhani zachitukuko, ayambaso kukhala ndichikhulupiliro kuti dziko la Malawi pansi paulamuliro wawo litha kuyendetsa bwino ndalama.

“Kuvomerezedwa kwa ndalama zokwana US$88.3 million ndi bungwe la International Monetary Fund pansi pa ndondomeko ya Rapid Credit Facility (RCF), ndi nkhani yosangalatsa kwambiri ku dziko lathu. RCF yabwera munthawi yake pomwe chuma cha dziko lino chinavutika pankhani zosiyanasiyana, ngozi zachilengedwe komaso zina zadzidzi.

“Boma langa likuchitenga ichi ngati chipambano chomwe chikusonyezo kubwezeretsedwa kwa chikhulupiliro kuchokera ku mabungwe akunja osiyanasiyana omwe pano akutha kuzindikira kuti dziko la Malawi likukhazikitsaso ndondomeko za zachuma zomwe cholinga chake ndi kufuna kupititsa patsogolo nkhani za zachuma,” atelo a Chakwera.

Iwo atiso boma lawo lipitilira kulumikizana ndi ma bungwe akunja osiyanasiyana amaiko akunja ndi cholinga chofuna kupeza njira zothetsera mavuto azachuma mdziko muno.

Pakadali pano, anthu mdziko muno kuphatikizapo wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima, ayamikira a Chakwera komaso nduna ya zachuma a Sosten Gwengwe kaamba kakhama lomwe ati lathandizira kupeza ndalamazi kuchokera ku bungwe la IMF.

A Chilima omwe anayankhula za nkhaniyi kudzera pa tsamba lawo la fesibuku, ati ndizoyenera kuti anthu aziyamikira komanso kusangangalala pomwe zabwino zikuchitika ndipo ati iyi zimasonyeza kuti pali kusintha maganizo pakati pa anthu.

Advertisement