A nthambi ya ndende ati vuto la chakudya lachepa tsopano

Advertisement

Mneneri wa nthambi ya ndende a Chimwemwe Shaba ati pakadali pano tsopano vuto lakusowa kwa chakudya mu ndende lachepa chifukwa ali ndi chakudya maka chimanga chomwe chikhoza kuwafikitsa mu March chaka chamawa.

Malingana ndi a Shaba, Boma lalowererapo pothetsa vuto lachakudya lomwe linalipo mndende za mdziko lino pofunsa bungwe la Admarc kuti ligulitse matumba 25,000 achimanga ku mthambi ya ndende.

“Ndizoonadi tinali ndivuto lazakudya mwezi wathawu, koma tinene kuti zinthu zimenenzo pakali panopa zinatha nkhani makamaka ya chimanga, chifukwa chakuti boma linalowererapo polamula bungwe la Admarc litigulitse matumba achimanga okwana 25,000 omwe tinagawa mndende zanthu kutengera ndi mmene ndende iliyonse imafunira.

“Ndipo tikhoza kufika mu March chaka chammawa vuto limeneli tidakalibe mwina tizingoyang’ana zinthu ngati ndiwo, mchere, shuga ndi zina” anatero a Shaba.

Pankhani yokhudza maganizo omwe anthu ambiri akhala akupereka kuti ndende za mdziko lino zilimbikitse ntchito yolima pazokha kuti azikhala ndi chakudya posadalira boma kuti liwagulire, a Shaba anati ndende zimalima kale pazokha koma pakadali pano ali ndi ganizo lolimbikitsa ulimi wamakono komanso wamalonda.

“Maganizo amenewo ndi abwino kwambiri ndipo tiyamikire kuti anthu ali ndi chidwi kuti ku Malawi Prison Service tizilima, sizimakhala bwino kuti tili ndi akaidi koma tizipempha zakudya, tingowukumbutsa mtundu wa a Malawi kuti ife kulimako timalima kale ndi kale.

“Tili ndi ofesi yapadera ya farms and industry yomwe imaona zaulimi ndipo tili ndi minda ikuluikulu ku Mpyumpyu prison, ku Domasi, Mikuyu 1 komanso 2, ku Mwanza, Rumphi Kambirambavi, Mzimba ndi ku Kasungu ndipo tikunena panopo tapeza malo ku Mzimba okwana 500 hekitazi komanso 100 hekitazi ina ku Kasungu.

“Ndipo chaka chino tinakatha kukhala ndi chimanga chokwanira kudyetsa ma prison kwa miyezi 6 koma mwina zinatikanika ndichifukwa chake tikufuna ulimi wanthu tiwulimbikitse tipeze malo ambiri komanso ulimi wathu ukhale wamakono komanso wamalonda,” anaonjezera motero a Shaba.

Masiku apitawa, ma lipoti amaonetsa kuti mu ndende pafupifupi zonse za dziko lino akaidi akumangodya phala komanso nyemba kutsatira kusowa kwa chakudya chifukwa anthu amalonda omwe amaperekera zakudya mundende anayamba kuperekera moperewera komanso ena anasiya kumene chifukwa panali kusamvana pankhani ya mitengo pomwe iwo amafuna nthambiyi ikweze mitengo yomwe imagulira chakudyachi.

Advertisement