Chakwera awowozedwa ku Lilongwe

Advertisement

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera awowozedwa ku Lilongwe pomwe amadutsa pa malo othilira mafuta a galimoto.

A Chakwera anali pa mdipiti wa galimoto pomwe anadutsa pa malo ena ogulitsira mafuta lero. Pamalowa panali gulu la anthu lomwe limadikira kuti lipeze mwayi ogula mafuta omwe pakali pano akusowa.

Pomwe a Chakwera amadutsa, anthu anayamba kuwawowoza ndipo ena amayankhula monyoza.

Malingana ndi kanema yemwe akuyenda pa masamba a mchezo, anthu omwe amawowozawa amafunsana ngati a Chakwera amaona zomwe zimachitika pamalowa.

Poyankhulapo pa masamba mchezo, aMalawi ena ati anthuwa sanalakwise kumuwowoza mtsogoleri wa dziko linoyu popeza anthu atopa ndi mavuto omwe alipo monga kukwera mitengo kwa zinthu ndi kusowa kwa mafuta.

Pansi pa ulamuliro wa a Chakwera, amabizinesi akudandaula kuti sizikuyenda, ndalama zakunja zikusowa, ntchito zikusowa komanso mitengo ya zinthu ikupitilirira kukwera.

Koma ena ati sibwino kumawanyoza a Chakwera popeza ndi mtsogoleri wa dziko lino ndipo amafunika ulemu.

Follow us on Twitter:

Advertisement

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.