Disembala mafuta afika K900 — atero a Gwengwe

Advertisement

Pomwe anthu m’dziko muno analonjezedwa kuti vuto la kuthimathima kwa magetsi litha mwezi wa Disembala chaka chino, nduna yazachuma yati anthu ayembekezeso kuti mafuta agalimoto atsika mtengo kufika pa K900 mwezi omwewu.

Nkhaniyi ikutsatira kutsitsidwa mtengo kwa mafuta a petulo omwe pano lita imodzi ikugulitsidwa pa K1746 kuchoka pa K1946 ndipo gasi ali pa K2600 kuchoka pa K2726 pa kilogalamu imodzi koma mtengo wa parafini ndi dizilo sunasinthe

Potsatira nkhaniyi, nduna ya zachuma a Sosten Gwengwe ati nkhaniyi ndiyosangalatsa kwambiri ponena kuti izi zikutanthauza kuti patha kukhala kusintha kwa mitengo ya zinthu zina mminsika.

Iwo ati pakadali pano boma lili kalikiliki kuonetsetsa kuti mtengo wa mafutawa agalimoto upitilire kutsikabe ndipo ati akufunitsitsa kuti pofika mwezi wa Disembala lita imodzi idzidzagulitsidwa pa mtengo wa K900.

“Mtengo wamafuta watsika. Nkhani yabwino.. Mitengo yakatundu wina ochuluka imadalira mtengo wa mafuta agalimoto. Tikugwira ntchito mosatopa kuti petulo azigulitsidwa pa K900 pofika mwezi wa Disembala,” atelo an Gwengwe omwe analemba pa tsambalawo la fesibuku.

Pakadali pano, anthu makamaka m’masamba amchezo ati akudikila mwachidwi kaamba koti boma lomweli lalonjezaso kuti vuto lakuthimathima kwa magetsi lomwe lilipo pano litha mwezi omwewu wa Disembala.

Pomwe mgwirizano wa Tonse umalowa m’boma, mtengo wamafuta agalimoto unali pa K850 pa lita limodzi koma mtengowu wakhala ukukwera kufika pomwe uli pano zomwe akuluakulu aboma akhala akunena kuti ndikamba kankhondo yapakati pa Ukraine komaso Russia.

Advertisement