Bungwe la Mulhako ladzudzulidwa posaitana a Chakwera ku mwambo wa chikhalidwe

Advertisement

Oyankhulapo pa nkhani zochitika mdziko muno adzudzula bungwe la Mulhako wa Alhomwe chifukwa chosaitana mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ku mwambo omwe ukuyembekezera kuchitika pa 9 October, 2022 kwa Chonde ku Mulanje.

A Latina Matenje adzudzula zomwe zachitikazi chifukwa iwo akuona kuti zachitika pa zifukwa za ndale. A Matenje atsutsa zomwe akunena a Mulhako kuti mtsogoleri wa dziko lino sapita kumwambowu pachifukwa chofuna kupulumutsa ndalama.

“Sinkhani yoona kwenikweni yomwe ena akunena kuti nkuthandiza a pulezidenti kusaononga  ndalama. Nzachidziwikire kuti Mulhako wa Alhomwe uli ndi kutsutsana kwakukulu ndi Tonse Alliance chifukwa choti mwina umagwirizana kwambiri ndi chipani cha DPP zomwe sizabwino kwenikweni chifukwa mtundu wina uli onse uli ndi mamembala ku chipani chilichonse zomwe sizingakhale bwino kuti nkhani za mitunduzi tizizipititsa kumeneku,” anatero a Latina Matenje.

Iwo anaonjezera kuti zikanakhala bwino kwambiri mabungwe omwe akuimira zamitunduwo agwirizane kuti azikhala ndi tsiku losangalala zachikhalidwe.

Wapampando wa Mulhako wa Alhomwe kuchigawo chakummwera, Blessings Makwinja, ananena masiku apitawa kuti bungweli siliyitana a Chakwera ku chikondwerero cha Mulhako cha chaka chino pofuna kupulumutsa ndalama zomwe zimagwiritsadi ntchito a Chakwera akayenda.

Iwo anatinso izi zadza kamba kakuti mtsogoleri wa dzikoyu sakuonetsa chidwi chofuna kuthandizapo pa zovuta zomwe mtundu wa Alhomwe ukukumana nazo mdziko muno kuyambira pomwe boma linasintha mu June 2020.

Mwambo wa Mulhako wa Alhomwe umachitika chaka chilichonse kwa Chonde ku Mulanje ndipo pa tsikuli Alhomwe amasangalala pokudya zakudya za chikhalidwe chawo, kuvina magule ndi zina zambiri.

Follow us on Twitter:

Advertisement